Chichewa

Malingaliro a Khirisimasi

Listen to this article

Khirisimasi ndi Januwale
Zalowa m’manyumba (adalakwitsa ndi oimbayo osati in Tadeyo)
Zaseseratu!
Kwa amene adaliko nthawi imene Kennedy Ndoya, ankatchuka kuti Madolo akhoza kuyikira umboni kuti ikafika nyengo ya Khirisimasi ngati ino, nyimboyi siyimasowa pawailesi.
Abale anzanga, inde, iyitu ndi nthawi yachimwemwe, chisangalalo.
Ndimakumbuka nthawi imeneyo ndikadali kwathu kwa Kanduku nthawi ino ndiye kunkakhala kulima maganyu osati masewera kuti tipeze ndalama zosangalalira. Ndani safuna kudzipepesa.
“Ife ndiye tatsekera kale kuntchito. Tikayambanso ntchito chaka cha mawa,” adatero mkulu amene adali ndi Abiti Patuma.
“Koma phwando la kuntchito kwanu lija ndiye ndewu zinaliko. Majuniyo kuswana ndi mabwana. Chikondi nacho chinali kuonetsedwa pakati pa majuniyo ndi mabwana awo pamdima komanso m’galimoto,” adatero Abiti Patuma.
Pajatu Abiti Patuma samayimva nkhani ya maphwandoyi. Ndithu pakadalipano sindikudziwa kuti chaka chino walowa m’maphwando a makampani angati!
“Iwe phwando la kuntchito, ngati sunafike pomenyana ndi abwana wako ndiye kuti phwandolo silinathe,” adatero mkulu uja.
“Koma kunavuta zedi. Abwana kuvina ndi sekilitale, mkazi wabwana zibakera mwa sekilitale! Ngodya zomanga phwando la kuntchito,” adatero Abiti Patuma.
“Ukudziwa kale. Kumwa zimene sunamwepo. Kusakaniza zakumwa. Ngati sudzimbidwa ndi nyama yootcha ndiye kuti kuphwandoko sunapiteko,” adabwekera Gervazzio.
Nkhani zili mkamwa, adatulukira mnyamata atavala malaya a blue, ojambulapo zitsononkho zinayi. Iye adali ndi chimwemwe kutsaya.
“Dizilo Petulo Palibe ndiye mafumu! Lamulo lolola Paparazzi ndi anzake kupeza mauthenga mosavuta yadutsa mu ulamuliro wa Moya Pete, adadi,” adatero mkulu uja.
Abiti Patuma adangoti kukamwa yasaaa!
“Ndipo Male Chauvinist Pigs isachite matama ngati idakambapo kanthu zopatsa ufulu Paparazzi ndi anzake,” adapitiriza.
“Kodi mkulu, si Dizilo Petulo Palibe yomweyo imene idasintha zina ndi zina lamulolo lisanalowe m’kanyumba komata? Si inu nomwe mudasintha lamulolo kuti zinthu zizikukomeranibe pomwe mukulamula, mwaiwala kuti zidzakugwirani pakhosi mukadzasiya kulamula pano pa Wenela?” adafunsa Abiti Patuma.
“Koma zonse zili apo, kudutsa kwa lamulolo kapena ayi, kwa ine palibe kusintha. Lamulo si lamulo basi? Lamuloli lidzachititsa kuti kukhazikitsidwe Public Information Commission yoti izidzathandizira kukwaniritsa lamuloli.
“Kunjakutu kuli Human Rights Commission, koma ufulu wa anthu siukuphwnyidwa?” adfunsa mkulu adali ndi Abiti Patuma uja.
Palibe chimene ndidatolapo!
Khirisimasi yabwino nonse!
Ine ndiye ndagwira bango, madzi awa sanditenga msanga. n

Related Articles

Back to top button