Chichewa

Malingaliro Potsegulira sukulu

Listen to this article

Dziko la Malawi latekeseka ndi nkhani yotsegulira sukulu ndipo pofuna kuonetsetsa kuti miyoyo ndi yotetezedwa komanso ufulu wa ophunzira usapitirire kuponderedzedwa, akatswiri aunikira momwe boma lingayendetsere ndondomeko yotsegulira sukulu.

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera adalengeza Loweruka kuti sukulu zonse zitsegulidwa kumayambiliro kwa mwezi wa September ndipo nthambi ya zamaphunziro mu komiti yoyendetsa za Covid-19 idatulutsa ndondomeko zoyenera kutsata potsegulira sukuluzo.

Mongokumbutsanapo, boma lidatseka sukulu zonse mwachikhadzakhadza m’mwezi wa March 2020 mliri wa Covid-19 usanafike m’dziko muno ndipo kaamba ka tchuthi chosakonzekerachi, zambiri zachitika zosokoneza maphunziro aana.

M’sukulu zambiri ana amakhala mothinana

Kadaulo pa zamaphunziro m’dziko muno Steve Sharrah wati ndondomeko zomwe boma lakhazikitsa n’zabwino koma zikusowekera kuunikira kochuluka kuti pologalamu yotsegulira sukulu ikhale yogwira ndi yaphindu.

Mwa zina, Sharrah wati ndondomekoyo siyikunena kuti sitepe iliyonse paulendo okatsegulira sukulu izitenga nthawi g yayitali bwanji polingalira kuti kwangotsala sabata ziwiri zokha kuti tifike sabata yoyamba ya September.

“Pali zambiri zofunika kuchitika monga aphunzitsi kukonzekera, sukulu zina zifunika kukonza zina ndi zina zisadatsegulidwe komanso pakunenedwa za zipangizo zosambira mmanja zomwe zifune ndondomeko yayitali yogulira katundu waboma. Pamenepa sipadaunikiridwe bwino kuti payenda bwanji,” watero Sharrah.

Iye watinso komiti yoyendetsa za Covid-19 yati sukulu zonse zikuyenera kuyenderedwa ndikutsimikizidwa kuti ndiyoyenera kutsegulidwa koma potengera kuchuluka kwa sukulu m’Malawi muno, nyengo yomwe boma lapeleka ndiyochepa kwambiri.

“Mwachitsanzo, mdziko muno muli sukulu za pulaimale 6 300 za boma ndi zoima pazokha komanso sukulu 1 400 za sekondale. Zonsezi zikufunika kuunikidwa zisadatsegulidwe koma ndi nthawiyi zukayikitsa,” watero Sharrah.

Iye adaonjeza kuti ganizo lophunzilira pabwalo popita mphepo silikuganizira za kusinthasintha kwa nyengo komwe kungasokonezenso maphunziro posachedwapa.

“Nanga titati tatsegulira maphunziro kenako nkuyamba mvula tidzatsekenso sululu? Apapa chikufunika ndikugwiritsa ntchito Covid-19 ngati phunziro lalikulu kuti tikonze maphunziro athu,” watero Sharrah.

Koma kadaulo pa zamaphunziro m’maiko osiyanasiyana Rob May wati Malawi watsopano ali ngati namwali yemwe tsogolo lake ndilowala ndipo asalole kuti Covid-19 apondeledze unamwaliwo.

May adati anthu asayembekezere kuti Covid-19 itha mwadzidzidzi kotero ganizo lotsegulira sukulu ndilabwino bola ngati ndondomeko zopewera zili zomveka.

“Maphunziro ndi kabali wotsegulira chitukuko cha dziko la Malawi ndipo kafukufuku wa Cambridge University adapeza kuti kulekelela maphunziro kukhoza kusokoneza chuma kwa zaka 65 zikubwerazo.

“Bungwe la Save the Children lidapeza kuti ana oposa 10 miliyoni akhonza kusiyira sukulu panjira chaka chino chokha ndipo izi zisokoneza chuma cha anawo pamoyo wawo wonse ndi $10 triliyoni,” adatero May.

Iye adati kuchedwetsa kutsegulira sukulu ndi mlozo wa chiwonongeko koma adawonjeza kuunikira kuti n’chofunikiraso kwambiri kuti miyoyo ya ana ndi aphunzitsi ndiyotetezedwa.

Koma eni sukulu zomwe sizaboma ati ndi wokonzeka kuti sukulu zikamatsegulidwa akhale ndi zonse zoyenera kuti akayamba kuphunzitsa asadzayimenso kaamba ka Covid-19.

“Talankhula kale ndi mamembala athu ndipo atsimikiza kuti agwirizana ndi ganizo lotsegulira sukulu ndipo atsatira zonse zomwe ndondomeko ikunena,” watero mkulu was bungwe la eni sukulu zomwe sizaboma Peter Patelo.

Makolo omwe achezako ndi Tamvani ati pempho lawo ndiloti boma lipange zotheka kuti anawo akabwerera kusukulu akakhale otetezedwa mokwanira.

Ena mwa makolowo ati likhoza kukhala ganizo labwino kugawa anawo mmagulu angapo kuti azipita kusukuluko ana ochepa panthawi imodzi ndicholinga chotsatira lamulo logonjetsera Covid-19.

Related Articles

Back to top button
Translate »