Nkhani

Malonda a chamba avuta ku Nkhata Bay

Listen to this article

Zikuoneka kuti chamba (ena amati kanundu) ndi malonda otentha m’boma la Nkhata Bay. Chaka chatha chokha anthu 25 adapezeka ndi milandu yokhudza katunduyu moti ngakhale chaka chino sichinathe, milandu 17 yokhudza chamba yapalamulidwapo kale.

Mlandu wauwisi ndi wa mayi wa zaka 34, Angela Banda, yemwe adapezeka ndi zikwama ziwiri zikuluzikulu zodzadza ndi chamba pa Roadblock ya Mukwiya m’bomali. Banda adakwera basi pa Dwanga ulendo wa ku Mzuzu sabata yathayi. Mwatsoka, ulendowu udathera m’manja mwa apolisi.

Katundu wovuta: Apolisi atagwira galimoto yonyamula shuga ndi matumba a chamba

Banda amachokera m’mudzi mwa Msomba kwa mfumu yaikulu Mabuka m’boma la Mulanje.

Malinga ndi mneneri wa polisi m’bomali, Ignatious Esau, anthu a zaka zosapitirira 30 ndiwo akupalamula kwambiri.

Esau adati malondawa akhoza kukhala otentha chomwechi m’bomali chifukwa ndi limodzi mwa maboma omwe amakopa kwambiri alendo kaamba ka nyanja.

“Komanso tikuona ngati chifukwa bomali lili m’malire a dziko lino ndi la Mozambique, choncho izi zitha kukhala zothandizira popititsa patsogolo malonda oletsedwawa,” adatero Esau.

Iye adati ngangale zili chomwechi, apolisi akuona kusintha.

Malinga ndi Esau, chiwerengerochi chatsikako pang’ono kaamba koti nawo mabwalo a milandu alowererapo tsopano.

“Mabwalo athu akuperekano chigamulo chokhwima kwa onse opezeka ndi mlandu wokhudza chamba,” adatero Esau.

Iye adati zafika poti apolisiwa akumayendanso m’sukulu kuphunzitsa ana za kuipa kosuta kanundu.

Malamulo a dziko lino, salola kubzala, kugulitsa kapena kusuta chamba ndipo aliyense wogwidwa akuchita izi amazengedwa mlandu mogwirizana ndi gawo 4a lowerengedwa limodzi ndi Lamulo 19 (ndime 1 ndi 2) la mankhwala oopsa.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »