Editors Pick

Malonda a fodya aliritsa alimi ena

Listen to this article

 

Chikadakhala chimanga bwenzi akusimba lokoma, koma poti ndi fodya oyimba adalasa ponena kuti ikulirenji ntchito, chaka ndi chaka alimi kwawo n’kulira. Zaoneka chaka chinonso pomwe alimi ambiri ali manja m’khosi ulendo wobwerera kumudzi fodya atavuta malonda kumisika ya okushoni.

Mmodzi mwa okhudzidwa ndi kuyenda udyo kwa malonda a fodya chaka chino, William Khudze, wa ku Magwero m’boma la Lilongwe, akuti iye adatenga ngongole kukalabu kuti agule feteleza ndi zipangizo zina za kumunda kupatula antchito omwe amamuthandiza kumundako ndipo amayembekezera kuti akagulitsa fodya wambiri, adzathana ndi nkhani zonsezi.Drying_tobacco

Iye akuti mpaka pano ngongoleyo sinabwezedwe komanso sanalipire antchito ake ngakhale kuti akuyembekezera kugwira nawonso ntchito chaka chino.

“Ndikunena pano, ndili ndi ngongole yoti ndilipire antchito koma ndalama palibe. Tidayamba kale kugwira ntchito ina pokonzekera ulimi wa chaka chino ndi chikhulupiriro choti mwina ziyenda, koma mmene zililimu tsogolo palibe apa. Fodya wanga sadagulidwebe,” adadandaula motere Khudze.

Malingana ndi bungwe loyendetsa za malonda a fodya la Tobacco Control Commission (TCC), msika wa fodya ukuyenera kutsekedwa mwezi ukubwerawu, makamaka pa 2 December, koma galimoto zonyamula fodya zikadali ngunda kumisika pomwe fodya wina akusowa malo osungirako m’midzi.

Msika wa fodya umayenera kutha sabata 25 ukatsegulidwa koma chaka chino boma lidakambirana ndi makampani ogula fodya kuti awonjezere nyengoyi ndi sabata 11 kuti alimi apeze danga logulitsa fodya yemwe adali asadagulidwe.

Pakutha kwa sabata 25 chitsegulireni msika chaka chino, alimi ambirimbiri adali asadagulitse fodya wokwana makilogalamu 20 miliyoni ndipo ngakhale nyengoyi idawonjezeredwa, alimi ambiri, monga Khudze, akulirabe ndipo pano ataya chiyembekezo kuti ulimi wa fodya uwapindulira.

Koma unduna wa zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi wati vutoli ndi lobala okha alimi kaamba kolima fodya woposa mlingo womwe amayenera kulima malingana ndi chiunikiro cha boma komanso makampani ogula fodya.

Woyang’anira ntchito zamalimidwe mu undunawu, Grey Nyandule Phiri, akuti alimi amapatsidwa zitupa zolimira ndi kugulitsira fodya koma ambiri mwa iwo satsatira zomwe zitupazi zimanena ndipo mmalo mwake amalima fodya wambiri mobzola mlingo.

“Izi ndi nkhani zovuta chifukwa zonse zimatsalira boma. Mwachitsanzo, momwe zakhalira chaka chinomu, zidatengera boma kukambirana ndi makampani ogula fodya kuti awonjezere nthawi koma mtsogolo muno sizidzakhala choncho, ayi,” adatero Phiri.

Kuvuta kwa malondaku kwayimitsa alimi mitu kaamba kakuti ena akuti sakudziwa kolowera kukatenga ndalama zobwezera ngongole zomwe adatenga kumayambiriro a ulimi wa chaka chatha ndi kulipira antchito a kumunda.

Bungwe la alimi a fodya la Tobacco Association of Malawi (Tama) lidati alimi akuphunzitsidwa za ubwino wotsatira mlingo wa pachitupa kuti zomwe aona chaka chino zisamaonekeoneke.

Mkulu wa bungweli, Reuben Maigwa, adati chaka chino alimi ambiri adatsatira njira zomwe maiko ambiri amalimbikitsa ngakhale kuti malonda akhumudwitsa alimi ambiri.

“Tikayan’gana zofunikira zambiri, alimi adatsatira monga zokhudza kusiya kugwiritsa ana ntchito, kusaika mapepala ndi zinyansi zina m’mabelo komanso kugwiritsa ntchito ziguduli zoyenera,” adatero Maigwa.

Fodya ndiye mgodi waukulu wa dziko lino komanso anthu ambiri amapeza ntchito muulimi wa mbewuyi moti posachedwapa, nduna ya zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi, George Chaponda, adanena kuti dziko lino silingasiye kulima fodya ngakhale mabungwe ndi maiko ena ali pakampeni yofuna kuthetsa ulimi ndi kusuta fodya.

Related Articles

Back to top button
Translate »