Nkhani

Malonjezo ayamba kuoneka

Boma latsopano la Tonse Alliance layamba kukwaniritsa ena mwa malonjezo ake a panyengo ya kampeni ndipo pomwe akadaulo osiyanasiyana ayamikira izi, atinso boma lisadzabwerere mmbuyo.

Kukwaniritsidwa kwa malonjezowo kudayamba kuoneka Lachiwiri m’Nyumba ya Malamulo pomwe nduna yatsopano ya zachuma Felix Mlusu idalengeza bajeti yoyembekezera ya K722.4 biliyoni.

Chakwera adalumbira Lamulungu

Mlusu watcha bajetiyo dzina loti kutukula ntchito zaulimi ndi zipangizo zotsika mtengo chifukwa mtengo wa fetereza watsika kufika pa K4 495 pa thumba la 50Kg monga mwalonjezo ndipo alimi 3.5 miliyoni ndiwo akuyembekezeka kupindula.

M’dziko muno muli mabanja odalira ulimi okwana 4.2 miliyoni koma ndondomeko yakale ya sabuside inkakomera alimi 900 000 kapena 1.5 miliyoni akachuluka.

M’bajetiyo, boma lakonza zokwenza poyambira ndalama za malipiro apamwezi kuchoka pa K35 000 kufika pa K50,000 komanso kukwenza malipiro oyambira kudula msonkho munthu yemwe amalandira K35 000 tsopano malipiro ake awonjezekera ndi K15 000 yomwe ndiyokwanira kugula matumba atatu a fetereza pa mtengo wa K4 495 n’kukhalakonso ndi zolipilira wonyamula fetelezayo.malipiro kukutanthauza kuti

Chimodzimodzi kukweza malipiro oyambira kudula msonkho kufika pa K100 000 kupangitsa kuti anthu apulumutse K17 500 yomwe kale amadulidwa kutanthauza kuti nawo akhoza kugula matumba atatu a fetereza ndi ndalamayo.

Koma ngakhale izi zili n’kuthekera kogwedeza mapezedwe a ndalama za boma, akadaulo pa za msonkho ndi zachuma agwirizana nayo nkhaniyi.

Kadaulo wazachuma Gowokani Chijere Chirwa wati nkofunikira kwambiri kuti boma lapanga momwe lapangiramu potengera umphawi wa anthu ndipo wati kangachepe komwe anthu azipulumutsa nkochuluka akagwiritsa ntchito bwino.

Naye kadaulo pa zamisonkho Emmanuel Kaluluma wati ngakhale kukwenza malipiro oyambira kudula msonkho kukhudze katoleredwe ka misonkho, boma lapanga bwino kuganizira anthu.

“Misonkho ndi imeneyo ndipo ndiyofunikadi koma palibe nzeru kutolera ndalama kwa anthu nkuwasiya alibe pogwira chifukwa afa ndi njala,” adatero Kaluluma.

Mubajetiyo, boma laonjezera ndalama za thumba la ngongole za achinyamata kuchoka pa K15 biliyoni kufika pa K40 biliyoni komanso lati pofika mchaka cha 2021 likhala litatsegula mwayi 600 000 wa ntchito.

Kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu m’dziko Makhumbo Munthali wati boma layamba bwino pokwaniritsa malonjezo chifukwa ubale umakoma nchilungamo komanso kukhulupilika.

“Mukakumbukira tikucheza za kampeni ndidanenapo kuti andale azilonjeza zinthu zomwe angakwanitse chifukwa zomwezo zimadzasanduka adani awo mtsogolo maka pa kampeni ina ngati sadazikwaniritse,” adatero Munthali.

Naye George Phiri wodziwa za ndale wati boma likamapanga zinthu zokomera anthu ake, zinthu m’dziko zimayenda komanso dziko silichedwa kutukuka.

“Tamverani, anthu amadziwa kuti andale amasintha miyoyo yawo akakhala pampando ndiye kuti munthuyo asade kukhosi, pamafunika naye azimvako kukoma kwa dzikolo ngati momwe layambira bomali,” adatero Phiri.

Akadaulowa adagwirizana pa mfundo yoti bola bomali lisasinthe momwe layambiramu chifukwa likatero anthu atsimikiza kuti andale zawo nzimodzidi.

Related Articles

Back to top button