Nkhani

Malungo atheretu—Unduna

Listen to this article

Pamene dziko limakumbukira ntchito yothana ndi malungo Lachiwiri, boma la Malawi lati likuyesetsa kuti malungo m’dziko muno atheretu.

Bungwe la zaumoyo pa dziko lonse la World Health Organisation (WHO) lidapatula 25 April chaka chilichonse kukhala tsiku lokumbukira nthendayi, imene imatengera kuli chete anthu ambiri, makamaka amayi oyembekezera ndi ana a mu Africa.aria

Ndipo pamene mutu wa chaka chino ‘Kuthetseratu Malungo’ ukukhudza dziko la Malawi kwambiri, WHO idalengeza kuti dziko lino, limodzi ndi Kenya komanso Ghana, akhala maiko oyamba padziko lapansi kulandira katemera wa malungo kuyambira chaka cha mawa.

Woimira WHO pankhani yolimbana ndi malungo m’dziko muno, Wilfred Dodoli adati

ndondomeko ya katemerayu ndi yongoyesera chabe koma wati ali ndi chikhulupiliro kuti ndi wothandiza makamaka kwa ana.

“Uku n’kubowoleza chinsinsi chothana ndi malungo. Tikuyembekezera kuti ana 120 000 a pakati pa miyezi isanu ndi 25 m’madera osankhidwa alandira katemerayu,” adatero iye.

Unduna wa zaumoyo wati katemerayu athandiza kuchepetsanso imfa zodza ndi malungo ndi pafupifupi 40 pa imfa 100 zomwe zimagwa pakati pa ana ndi  chiyembekezo choti mtsogolo muno vutoli lidzatheratu.

Undunawu watinso wakhazikitsa kafukufuku wofuna kupeza momwe vuto la malungo lilili m’dziko muno pofuna kuonjezera mapologalamu ena oyenera kuti dziko la Malawi likwanitse cholinga cha mutu wa chaka chinowo.

Mkulu woyang’anira ntchito zaumoyo muunduna wa zaumoyo Dr Charles Mwansambo wati kafukufukuyu achitika m’madera osankhidwa ndipo achitidwa ndi madotolo omwe adaphunzitsidwa bwino ntchito ya zaumoyo makamaka zokhudzana ndi malungo.

“Kafukufukuyu akhudza kuunika kagwiritsidwe ntchito ka masikito otetezedwa, kaperekedwe ka thandizo la mankhwala a malungo, kuyeza malungo ndi kuchuluka kwa magazi m’matupi mwa ana omwe atenge nawo gawo mu kafukufukuyu,” adatero Mwansambo.

Mu uthenga wa tsiku lokumbukira matenda a malungo, unduna wa zaumoyo udati m’zaka zisanu zapitazi, imfa zodza ndi malungo zachepa ndi 60 pa imfa 100 zomwe zinkachitika ndipo undunawu wati ichi n’chifukwa cha kuyenda bwino kwa mapologalamuwa.

“Chifukwa cha mapologalamu monga kugawa masikito onyikidwa m’mankhwala, kupopera mankhwala m’makomo ndi kulimbikitsa amayi oyembekezera kuyezetsa malungo  ndi kulandira thandizo nthawi yabwino, imfa zodza ndi malungo zatsika,” chidatero chikalatacho.

Mkulu wa bungwe la zaumoyo la Malawi Health Equity Network (MHEN) George Jobe wati ndondomeko zomwe unduna wa zaumoyo uli nazo ndi zabwino.

Iye adati  njuga yagona pa momwe ndondomekozi zikuyendetsedwera ndi

maphunziro a zaumoyo omwe anthu akulandira kuti azitha kutsatira bwino ndondomekozi kuti zipindule.

“Ndondomekozi n’zabwino koma mpofunika kuunika kuti anthu akuphunzitsidwa mokwanira? Ndikunena izi polingalira zomwe zikuchitika m’maderamu kuti ena akugwiritsa ntchito masikito omwe amalandira powedzera nsomba ndi kupangira madimba,” adatero Jobe.

Senior Chief Mwadzama ya ku Nkhotakota idavomereza kuti pakadali vuto lalikulu pakati pa anthu kutsatira malangizo makamaka pakagwiritsidwe ntchito ka masikito a udzudzu ngakhale kuti pang’onopang’ono anthu ayamba kumvetsetsa.

“Poyamba kudali zikhulupiliro zoti mankhwala a masikitowa amafowola anthu koma pano ambiri akumvetsetsa kufunika kogona mmasikito. Tidakhazikitsanso malamulo kuti opezeka akugwiritsa ntchito masikito powedzera nsomba kapena kupangira dimba, tizimulambalala pakabwera mapologalamu ena ndiye anthu akuwopa,” adatero Mwadzama.

Padakali pano, nduna ya zaumoyo Peter Kumpalume yati dziko lino lasayina pangano ndi dziko la China kuti akatswiri a ku China abwere kudzathandiza pakafukufuku wa mankhwala a zitsamba ochiza malungo.

“Mankhwalawo alipo ndipo timawagwiritsa ntchito, koma tikufuna kupeza kuti mankhwala omwe angagonjetse malungo ndi ati ndipo tingawakonze bwanji m’mafakitale kuti akhale osavuta kugwiritsa ntchito,” adatero Kumpalume

Dziko la China lidagonjetsa kale malungo ndipo wachiwiri kwa nduna ya zaumoyo ndi kulera m’dzikolo Wang Guogiang adati izi zidatheka pogwiritsa ntchito mankhwala a zitsamba.

Related Articles

Back to top button
Translate »