Chichewa

Mameya afanana maloto

Listen to this article

 

Pamene chisankhocho cha mameya atatu a m’mizinda ya dziko lino chadutsa, masomphenya a mameya onse agona polimbikitsa kuteteza malo aboma, kutolera misonkho, kulimbikitsa chilungamo pa kayendetsedwe ka ndalama komanso chitukuko.

Sabata ziwiri zapitazi, kudali zisankho za mameya pomwe makhansala a mzinda wa Mzuzu adasankha William Mkandawire wa chipani cha PP kukhala meya pomwe ku Lilongwe adasankha Desmond Bikoko wa MCP ndipo ku Blantyre adasankha Wild Ndipo wa DPP.

Ngakhale akuluakuluwa ndi osiyana zipani, Tamvani wapeza kuti pomwe amavala mwinjiro wa ufumu wa mizindayi, onse maloto awo ndi amodzi, si dale zimene zidakuta zisankhozo.

Mameya onse atatu, amene adasankhidwa patatha zaka ziwiri ndi theka kuchokera pomwe adasankhidwira mu May 2014, adati masomphenya awo ali polimbikitsa kutolera misonkho ya khonsolo, kuteteza malo a makhonsolo, kulimbikitsa kayendetsedwe kolondola

Ku Lilongwe adasankha Bikoko

ka chuma cha khonsolo ndi kutukula makhonsolo awo.

Mmodzimmodzi mwa iwo adaonjeza kuti iyi si nthawi yoika manja kumbuyo.

“Mu teremu yoyamba, ine ndi a [meya opuma a Noel] Chalamanda tidapanga zambiri pomwe ndidali wachiwiri wawo. Pano, ngati khansala, ndipitiriza ntchito zimenezo komanso kuposerapo,” adatero Ndipo.

Bikoko adati: “Sindidabwere kudzasewera kapena kudzatamidwa koma kudzatumikira ndi kutukula khonsolo. Pali zambiri zomwe zikadachitika koma sizidachitike. Ntchito yanga ikhala kuchita zimenezo kuti khonsolo isinthe.”

Koma Mkandawire, yemwe ndi yekhayo amene sadalandidwe mpando wa umeya adati: “Ntchito ndi zomwe ndidayamba kale ndipo anthu akuzidziwa nchifukwa chake andipatsanso mwayi wina owatumikira. Ndikufuna kuwatsimikizira anthu a m’khonsolo ya Mzuzu kuti ntchito zomwe ndidayamba zipitilira,” adatero Mkandawire.

Ndipo wa ku Blantyre

 

Ndipo adangonjetsa bwana wake Chalamanda oima payekha pa chisankho chimene chidadzidzimutsa ena. Ndipo chisankho cha ku Lilongwe chidadza ndi kathumba pomwe yemwe adasankhidwa kukhala wachiwiri kwa meya, Juliana Kaduya, adazimirira ati chifukwa amaopsezedwa.

Juliana, yemwe ndi wa DPP adasinkhidwa ndi a MCP kuti ayimire pampandowo zomwe zidachititsa akuluakulu ena a DPP kuganiza kuti adali ndi kampeni kumphasa.

Akadaulo pandale ati kutayidwa kwa Chalamanda komanso kuzimirira kwa Kaduya kukusonyeza kuti ndale zidali patsogolo pa zisankhozo.

 

Mmodzi mwa akatswiri potanthauzira ndale, Boniface Dulani, adati zotsatira za ku Blantyre zidatengera ndale osati zintchito zamunthu.

“Pakuoneka kuti anthu asankha potengera chipani osati ntchito za munthu makamaka tikatengera chitukuko chomwe Chalamanda amachita mumzindawo,” adatero Dulani.

Katswiri wina, Mustafa Hussein, adadzudzula mchitidwe oopseza adindo monga momwe zidakhalira ku Lilongwe.

“Adindo sangakwaniritse masomphenya awo bwinobwino ngati akugwira ntchito mwamantha. Zisankho zatha, chofunika tsopano nkuvomereza ndikuwapatsa mpata omwe adapambana kuti agwire ntchito,” adatero Hussein.

Ma Mayor onse opuma m’makhonsolo a Blantyre ndi Lilongwe adalonjeza kugwira ntchito ndi omwe atenga mipandoyi. n

Related Articles

Back to top button