Nkhani

Mamonitala ena sakupezeka kolembetsa

Mamonita a zipani zina sakupezeka m’malo olembetsera mavoti, Tamvani wafukula.

Mmalo 7 a m’midzi yomwe Tamvani adazungulira mkati mwa sabatayi, malo amodzi okha a Kasambwe kwa T/A Kabudula ndiko kudapezeka monitala wa chipani cha People’s Party (PP) koma mmalo ena onse m’mangopezeka a zipani za Malawi Congress (MCP) ndi Democratic Progressive (DPP) basi.

Ansah: Tidauza zipani

Nkhaniyi yakhumudwitsa bungwe loyang’anira zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lomwe lati mchitidwe otere ndiwo umayambitsa kusakhutira ndi zotsatira za chisankho.

Mkulu wa MEC, Jane Ansah adati: “Tidapempha zipani zonse kuti zitumize mamonitala mmalo olembetsera kuti aziona momwe zinthu zikuyendera n’kupereka malipoti ku zipani zawo koma takhumudwa kuti zipani zina zilibe ma monitala,” Watero mkulu wa MEC Jane Ansah.

Malingana ndi bungwe lowona za momwe ndondomeko ya zisankho ikuyendera

la Malawi Electoral Support Network (Mesn), monitala ndi diso komanso khutu la chipani kapena bungwe lokhudzidwa pachisankho.

Mkulu wa bungwelo Steve Duwa adati monitala amayenera kukhala pamalo wolembetsera, kuvotera kapena kuwerengera zisankho ngati mboni ya chipani kapena bungwe lake ndipo amayenera kusayinira zotsatira pamapeto.

“N’kofunika kwambiri kuti chipani chikhale ndi monitala pa kalembera, chisankho kapena kuwerenga zotsatira ndipo amayenera kusayinira

pamapeto pake akakhutira kapena kukana ngati ali ndi umboni woti pena pake sipadayende bwino,” adatero Duwa.

Zipani zina zomwe zimayembekezeka kukhala ndi mamonitala ake mmalo olembetsera ndi United Democratic Front (UDF), Alliance For Democracy (Aford) ndi United Transformation

Movement (UTM).

Mneneri wa UTM, Joseph Chidanti Malunga adati m’sabatayi adaali kuthamanga zolembetsa gululo ngati chipani choncho sanatumize mamonitala.

“Malamulo amalola chipani chomwe chidalembetsa ndipo n’chodziwika kutenga nawo mbali, ife tidali tisadamalize mbali yolembetsayo koma mtsogolomu tizikhala nawo paliponse,” adatero Malunga.

Mneneri wa UDF Ken Ndanga adati asankhabe mamonitala mtsogolomu. Iye adati zimavuta kuika mamonitala mpaka pamene chipani chawo chidachititsa msonkhano wake waukulu.

Malinga ndi wofalitsa nkhani za PP, Noah Chimpeni, chipanicho chili ndi chikhulupiriro kuti mamonitala a mabungwe omwe siaboma agwira ntchito yoyenera.

Related Articles

Back to top button