Nkhani

Mandela adwala mwa kayakakaya ku South Africa

Listen to this article

Mtsogoleri wakale wa dziko la South Africa Nelson Mandela adali kudwalika zedi pachipatala china ku Pretoria m’dzikomo.

Pomwe timasindikiza Tamvani Lachinayi n’kuti Mandela akadali m’chipatala, kulandira chithandizo koma ali mwa kayakaya.

Makaziwe, mwana wamkazi wamkulu wa Mandela, Lachinayi adati bambo wake adakali moyo, ndipo adadzudzula atolankhani akunja kwa dzikolo posalemekeza Mandela pomwe akudwala. Atolankhaniwo adali unjiunji kunja kwa chipatalacho kufuna kumva ngati Mandela, yemwe omukonda amamutcha Madiba, watisiya.

“Kunena zoona, atate wanga sali bwino, koma akadali moyo. Tikawalankhula akumatsegula maso ndi kutiyang’ana. Akadali moyo,” adatero Makaziwe.

Iye adati si bwino kuti atolankhani a maiko ena azifalitsa nkhani zosayenera za kudwala kwa Mandela. Adanena izi wailesi ya kanema ina itaulutsa kuti Mandela amathatha ndipo adali pamakina oonjezera moyo.

“Ngati amanena kuti amalemekeza Mandela, bwanji sakuonetsa izi m’zochita zawo? Pomwe nduna yaikulu yakale ya ku Britain Margaret Thatcher amadwala, sitidapite kuchipatala kwake kukamusuzumira,” adatero Makaziwe.

Mandela, yemwe adabadwa zaka 94 zapitazo, adadziwika dziko lonse malinga ndi nkhondo yake yothana ndi tsankho m’dzikolo. Izi zidachititsa kuti amangidwe ndipo adakhala m’ndende zaka 27. Atangotuluka kundendeko adasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dzikolo mu 1990, koma pamene ambiri amayembekezera kuti abwezera nkhanza kwa azungu chifukwa cha ulamuliro wawo wa tsankho, iye adalalika za chiyanjano ndi chikhululukiro pakati pa mitundu ya anthu onse am’dziko la South Africa.

Atangolamulira zaka zisanu, adazisiya.

Related Articles

Back to top button
Translate »