Nkhani

Maofesala a kalembera ayera mmanja

Listen to this article

Maofesala omwe akugwira ntchito yolembera nzika za dziko lino m’nkalembera wa anthu mwaunyinji ayamba kulandira malipiro awo atsopano.

Chiyambireni ntchitoyi mwezi wa May chaka chino, maofesalawa akhala akudandaula ndi kuchepa kwa malipiro awo omwe adali pa K5 600 pa tsiku.

M’kulira kwawo, maofesalawa amati ndalamayo siyikugwirizana ndi momwe katundu wakwerera m’dziko muno.

Pachifukwachi, ogwira ntchitowa akhala akuopseza kuti anyanyala ntchito ngati malipiro awo sakwera kufika pa K10 000 patsiku, kutanthauza kuti ndalamayi njokwana K250 000 pa gawo lililonse la ntchitoyi.

Pachiyambi, maofesala ongogwirizirawa amalandira K120 000 pa gawo lililonse pomwe owayang’anira amalandira K150 000 ndipo ndalamayi idaonjezeredwa kufika  pa K175 000 ndi K205 000 mwa ndondomeko yomweyo.

Ndipo kuopsezaku kudapherezera sabata ino pomwe maofesalawa adanyanyaladi ntchito kwa masiku awiri ngakhale chifukwa chenicheni chidali chokakamiza boma kutulutsa anzawo 14 omwe adatsekeredwa m’chitokosi cha apolisi mumzinda wa Mzuzu la Mulungu lapitali.

Nduna ya za chitetezo Grace Chiumia ndiyo idalamula apolisi kutsekera anthuwa itawapeza atasonkhana pa Shoprite ya mzindawu kukambirana zokhudza ndalama yapamwambayi.

Anthuwa adatulutsidwa Lolemba lapitali pa belo ya polisi.

Mneneri wa bungwe loyendetsa ntchito ya kalemberayu la National Registration Bureau(NRB), Norman Fulatira, adauza Tamvani Lachitatu kuti mavutowa athana nawo chifukwa bungwe la United Nations Development Programme (UNDP) layamba kupereka ndalama zapamwambazi zomwe lakhala likulonjeza kuchokera mwezi wa May.

“Ndalama za ofesalawa aliyense zidakwera ndi K55 000 kuyambira gawo lachiwiri la kalemberayu lomwe lidayamba mwezi wa June,” adatero Fulatira.

Iye adaonjeza kuti kunyanyala ntchito kudatha chifukwa  padali mgwirizano pakati pa maofesalawa ndi UNDP kuti ilipire ndalama zapamwamba zonse m’masiku anayi; ndipo ntchitoyi idayamba lachiwiri.

Iye adati kunyanyala kwa ntchitoku kwakhudza ntchito ya kalemberayu koma kuti kunyanyalaku kwakhudza kwakukulu bwanji ntchitoyi, zioneka masiku 25 akadutsa.

Pakadali pano ntchitoyi ikulowa m’gawo lachisanu lomwe muli maboma a Mzimba, Rumphi, Karonga, Chitipa ndi Nkhata Bay.

Anthu pafupifupi 6 miliyoni ndiwo alembetsapo, chiyambireni cha kalembera wa unzika m’dziko muno. n

Related Articles

Back to top button