Matola akuchulukitsa ngozi pamsewu

Apolisi ati miyoyo ya anthu ikupululuka kaamba ka matola omwe akuchulutsa ngozi pa msewu.

Malingana ndi chikalata chomwe apolisi atulutsa posachedwa, kugwiritsa ntchito galimoto zonyamula katundu potengera anthu ku masewero, ukwati, maliro si kovomerezeka.

Kukwera matola n’kuyika moyo pa chiswe

Chikalatachi, chomwe wasayinira ndi mneneri wa polisi m’dziko muno James Kadadzera, chikukumbutsa madalaivala kuti aziyendetsa anthu pa galimoto zoyenera monga maminibasi ndi mabasi.

“Ndi udindo wa anthu kutsatira malamulo apa msewu kuti ngozi zichepe m’dziko muno. Galimoto za matolazi zikachita ngozi, miyoyo ya anthu imakhala yosatetezeka,” iye adatero.

Kadadzera adachenjeza madalaivala omwe apange zosemphana ndi malamulo a pamsewu kuti alandira chilango.

“Ku ukwati kapena ku maliro, tigwiritse ntchito mabasi poteteza miyoyo ya anthu. Koma pomwe malore ndi matiraki ndi njira yokhayo yamayendedwe, tikatenge chilolezo ku Road Traffic Directorate osati ku polisi,” iye adatero. 

Related Articles

Back to top button