Nkhani

Maudindo ayamba kuchucha m’boma

Listen to this article

Pomwe mtsogoleri wa dziko lino yemwe wangosankhidwa kumene Lazarus Chakwera wayamba kusankha adindo m’bom, ku Nyumba ya Malamulo zinthu zasadabuzika.

Chakwera adayamba n’kusankha nduna zisanu zomwe ndi wachiwiri wake Saulos Chilima ngati nduna ya mapulani a zachuma ndi woyang’anira za ogwira ntchito m’boma, Felix Mlusu ngati nduna ya zachuma.

Adakana unduna: Msishakuchoka

Iye adasankhanso Richard Chimwendo Banda ngati nduna ya chitetezo cha m’dziko komanso Modecai Msisha ngati nduna ya za malamulo ndi chilungamo ndinso Chikosa Silungwe ngati mlangizi wamkulu wa boma pa malamulo. Koma Msisha adakana udindowo.

Pambali pa awa, Chakwera adasankhanso Prince Kapondamgaga ngati woyang’anira ogwira ntchito ku nyumba ya boma, Zangazanga Chikhosi ngati mlembi wamkulu wa boma komanso Janet Banda ngati wachiwiri wake.

Chakwera adati pali chikonzero choti asankhe nduna zosaposa 30, pomwe nduna zosachepera 12 zikhale amayi.

Ku Nyumba ya Malamulo nako kudachitika pelete pomwe omwe adali kutsogolo, lero ali kumbuyo ndipo omwe atsogolera, pano akutsatira.

Maudindo m’nyumbayo adasintha moti yemwe adali mtsogoleri wa nyumba yonse Kondwani Nankhumwa pano ndi mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma pomwe Chimwendo Banda yamwe adali mbali yotsutsa boma pano ndi mtsogoleri wa nyumba yonse ndipo akukhala mpando oyambilira m’nyumbayo.

Bright Msaka ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa DPP Nankhumwa, Simon Vuwa Kaunda ndi wokhazikitsa bata kumbali ya DPP pomwe Mary Navicha ndi wachiwiri wake.

John Chikalimba ndi mtsogoleri wa chipani cha PP, Noah Chimpeni ndi okhazikitsa bata ku mbali ya PP pomwe Ackson Kalaile Banda ndi wachiwiri kwa Chimpeni.

Tsopano nyumbayi ikukonzekera zosintha utsogoleri wa makomiti ena kuti zigwirizane ndi momwe malamulo akagwiridwe kantchito m’nyumbayo amanenera. Malinga ndi malamulowo, apampando a makomiti sayenera kukhala ochokera kuchipani cholamula choncho makomiti onse amene wapampando ndi wachipani cha MCP tsopano asintha.

Chimwendo Banda adati ngati mtsogoleri wa nyumba yonse, aonetsetsa kuti aphungu akutsatira malamulo a nyumbayo komanso kuti zochokera m’nyumbayo zizikhala zokomera anthu.

“Paja nkhani ndi ya tsogolo lowala ndiye kuwalako kukuyenera kuyambira kwa adindo ngati ife choncho ndionetsetsa kuti ndigwire ntchito ndi aphungu onse kuti titumikire Amalawi,” adatero Chimwendo Banda.

Related Articles

Back to top button