Chichewa

Maule akusambabe wamkaka

Listen to this article

 

Khomo la ukwati silisowa. M’banja la Nyasa Big Bullets kudakali chisangalalo kutsatira chipambano chawo pobabata asilikali a ku Mzuzu, Moyale Barracks.

Inde ndi asilikali, koma Loweruka lapitali adalira ndi kukukuta mano atadzidzimutsidwa ndi Bullets yomwe idachita ukali kumapeto kwa masewerowo pamene Moyale imafuna iyambe kusangalala.

Ichotu chidali chikho cha Presidential Cup chomwe wopambana adatenga K10 miliyoni ndipo wogonja kutenga K5 miliyoni.

Moyale idachinya pa mphindi 38 m’chigawo choyamba kudzera mwa Wiseman Kamanga. Idalimba poteteza chigolicho mpaka mphindi 90 m’chigawo chomaliza.

Ochemerera Bullets kusamba mkaka
Ochemerera Bullets kusamba mkaka

Goloboyi wa Moyale, Juma Chikwenga ndi osewera onse a Moyale adayamba kupha nthawi apo woimbira Duncan Lengani akuganiza zothetsa masewerowo ikangotha nthawi yoonjezera.

Mpanipani udali ku Bullets ndipo mphunzitsi wawo Franco Ndawa adalowetsa osewera kutsogolo anayi; Chiukepo Msowoya, Diverson Mlozi, Mussa Manyenje ndi Aimable Nikiyiza ndipo Bullets imadza ngati mbandakucha.

Patatha mphindi 93, wosewera wa Moyale adachita theng’eneng’e mpaka kugwira mpira kupezetsa Bullets penote ndipo Msowoya adachinya kuti masewerowo alowe m’mapenote.

Pilirani Zonda ndi Msowoya adaphonya mapenote a Bullets pamene Yamikani Fodya, Miracle Gabeya, Nikiyiza ndi Fisher Kondowe adachinya.

Love Jere ndi Chrispine Fukizi a Moyale adagwiritsa mapenote awo ndipo Sandress Munthali, Mtopijo Njewa ndi Timothy Nyirenda adamwetsa. Boy Boy Chima adamenyetsa chitsulo kupangitsa kuti Maule atenge chikhochi.

Ochemerera Bullets adayenda ndi mimba, ena kuvula zovala ndi ena kusamba mkaka kusangalala kuti timu yawo yatenga chikho. Osewera a Moyale adagwa pansi, kulira mosatonthozeka.

Fodya adati loto tsopano lasanduza zochitika, “Mulungu adali mbali yathu, zidali zovuta koma Mulungu wazitheketsa,” adatero iye.

Mphunzitsi wa Moyale adati woimbira sadali bwino: “Imene ija si penote, ndadabwa kuti nchifukwa chiyani woimbira adaimba pamenepo.” n

Related Articles

Back to top button
Translate »