Nkhani

Mavuto a madzi akula mu October ku Lilongwe

Listen to this article

Pomwe anthu mumzinda wa Lilongwe akubangula ndi vuto la kuzimazima kwa magetsi, kampani yopereka madzi ya Lilongwe Water Board yachenjeza kuti madzi nawo avuta mwezi ukudzawu.

Mneneri wa bungweli, Bright Sonani, watsimikiza za nkhaniyi koma wati anthu asade nkhawa kwambiri chifukwa madzi azitulukabe ngakhale mwa apo ndi apo.Women_Drawing_water

Sonani wati bungweli litulutsa ndondomeko ya mmene madzi azitulukira kuti anthu azitunga n’kusunga madzi okwanira m’makomo mwawo panthawiyi.

“Mwezi umenewu tikhala tikukonza ena mwa mathanki omwe timasungiramo madzi. Tikuchita izi malingana ndi kuti anthu ogwiritsa ntchito madzi akuchuluka ndiye tikufuna kukhala ndi mosungira mokwanira,” adatero Sonani.

Malingana ndi chikalata chomwe bungweli lasindikiza, madzi azidzasiya 6 koloko mmawa ndi kuyambanso kutuluka 6 koloko madzulo ndipo tsiku loyamba kusiya ndi Lolemba pa 28 September.

Potsirapo ndemanga, wapampando wa mabungwe a anthu ogwiritsa ntchito madzi mumzinda wa Lilongwe, Bentry Nkhata, wati nkhaniyi ndi yoopsa polingalira kuti anthu amadalira madzi pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.

Iye adati madzi akasowa matenda, makamaka am’mimba monga kolera ndi kamwazi, amabuka kaamba koti anthu amamwa ndi kugwiritsa ntchito madzi osatetezedwa.

“Nkhani yowonjezera mosungira madziyo ndi yabwino chifukwa zikutanthauza kuti mtsogolo muno madzi sazidzavutavuta koma nkhawa ili pakuti anthu azigwiritsa ntchito chiyani? Nthawi zambiri madzi akasowa kumakhala mavuto aakulu,” adatero Nkhata.

Unduna wa zaumoyo wati nkhaniyi isachititse anthu kutayirira ndipo wati chofunika n’kusunga madzi okwanira m’makomo mwawo kapena kugwiritsa ntchito njira zotetezera madzi.

“Pafupifupi m’dera liilonse muli alangizi a zaumoyo choncho tiyeni tonse tiziwafunsa momwe tingatetezere madzi kuti tipewe matenda am’mimba panyengoyi,” adatero mneneri wa unduna wa zaumoyo, Adrian Chikumbe.

Nthawi zambiri madzi akasowa, anthu amadalira zitsime kapena mitsinje yomwe madzi ake amakhala ndi dothi komanso tizilombo toyambitsa matenda am’mimba.

Related Articles

Back to top button
Translate »