Chichewa

Mayi akumuganizira Kupha mwana wake

Listen to this article

A polisi agwira sing’anga ndi mayi wina powaganizira kuti adapha mwana wa mayiyo wa zaka 11 ku Machinjiri mu mzinda wa Blantyre.

Malinga ndi mneneri wa polisi m’bomalo Augustus Nkhwazi, mayiyo Chifundo Matapira wa zaka 39, komanso sing’angayo Harrison Nyasulu wa zaka 33, akuwaganizira kuti adapha Tadala Matapira ndikukwilira mtembo wake mu mpanda momwe mayiyu amakhala.

Nkhwazi adati bambo ake a mwanayo Kondwani Matapira ndiye adadziwitsa apolisi za kusowa kwa mwana wake mwezi wa February chaka chino.

Bamboyu adauza apolisi kuti adapita ku Tanzania ndipo pobwerera mwana wakeyo sadamupeze.

Wojambula wathu kuganizira momwe zidalili mayiyu atamangidwa

“Titamufunsa mayiyu zomwe akudziwa pakusowa kwa mwanayu adatiyankha kuti akulandira chithandizo cha mankhwala kwa sing’anga,” adatero Nkhwazi.

Apolisi akhala akufunafuna sing’angayo, koma samamupezeka kaamba koti adathawa moti amugwira mwezi uno ku Uliwa m’boma la Karonga.

“Awiriwa atafunsidwa adaulula kuti adakwilira mtembo wa mwanayo pa August 8 mwezi uno mu mpanda wa Matapira ku Area 1, Machinjiri,” Nkhwazi adatero.

Apolisi afukula mtembowo ndi awutumiza ku chipatala cha Gulupu kuti adziwe chomwe chidapha mwanayo.

Matapira amachokera m’mudzi mwa Chidengu, Mfumu Timbiri m’boma la Nkhata Bay pamene Nyasulu amachokera m’mudzi mwa Mwakashunguli, Mfumu Mwerang’ombe m’boma la Karonga.

Related Articles

Back to top button
Translate »