Chichewa

Mayi amwalira kokafuna golide

Listen to this article

 

Mayi wa zaka 36 wamwalira ku Salima pamene dothi la mumtapo wa golide yemwe amafunafuna litamugwera iye ndi mwamuna wake.

grave

Mneneri wa apolisi ku Salima Gift Chitowe watsimikiza za nkhaniyi pouza Msangulutso Lolemba lapitali kuti nkhaniyi idachitika pa 8 January chaka chino pamene mayi womwalirayu, Elinati Mkaundu, pamodzi ndi mwamuna wake adanyamuka kumudzi kwawo kupita kumudzi wa Sadzu komwe ankafuna kukayesera mwayi wawo kokafuna miyala yamtengo wapatali yotchedwa galanayiti.

Chitowe adati atafika kumalo komwe kunali mtapoko mayiyo ndi mwamuna wake adafikira kulowa m’dzenje la mtapolo ndi kuyamba kufunafuna miyala ija koma mwatsoka dothi lomwe lidali mudzenjemo lidawagwera ndipo mayiyu adamwalira pomwepo pamene mwamuna wake adavulala thupi lonse ponyukanyuka.

Thupilo adalitengera kuchipatala chachikulu cha Salima komwe adakalipima ndipo zotsatira za kuchipatala zidasonyeza kuti mayiyu adamwalira chifukwa chobanika. n

Related Articles

Back to top button
Translate »