Nkhani

Mayiyo adamukhapanso m’mutu

Bwalo la milandu ku Mangochi lagamula dotolo wina kukasewenza kundende zaka 19 atampeza ndi mlandu wogwiririra wodwala.

A George Gwagwala a zaka 31 omwe amagwira ntchito yothandiza odwala pachipatala cha Mangochi adagwirira mayi wa zaka 20 komayambiriro kwa mwezi wa August.

Malinga ndi mneneri wapolisi m’boma la Mangochi, a Amina Daudi, mayiyo adapita pachipatalapo ndi vuto la mwendo.

Ndipo apa Gwagwala adauza mayiyo pamodzi ndi wodwala wina wamwamuna kuti amutsatire kumalo ake ogona.

“Dotoloyo adayamba kuthandiza wodwala wa mwamuna ndipo atamaliza, adaitana mayiyo m’chipindamo,” adalongosola a Daudi.

Iwo adati mayiyo adauza bwalo la milandu kuti dotoloyo adakhoma chipindacho ndi kumugwiririra mayiyo komanso adamuvulaza.

Malinga ndi a Daudi, mayiyo adakamang’ala ku bungwe la Youth Net and Counselling (Yoneco) omwe adakaitula m’manja mwa apolisi.

Daudi adati koma nkhaniyi itayamba kulowa kubwalo la milandu, a Gwagwala adaukana mlanduwo zomwe zidachititsa a boma kuitana mboni zinayi.

Koma a Gwagwala adapempha woweruza milandu Rodrick Michongwe kuti amuchitire chifundo chifukwa makolo ake adaononga ndalama zambiri pomuphunzitsa ndipo zilowa m’madzi akamtumiza kundende.

Popereka chigamulo, a Michongwe adati a Gwagwala akufunika chilango chokhwima kuti ena atengerepo phunziro.

A Gwagwala amachokera m’mudzi mwa Helemani, Mfumu Khwethemule, m’boma la Thyolo.

Related Articles

Back to top button