Chichewa

Mbali ina ya mnzinda wa Blantyre

Listen to this article

local-shops

Kunena zoona, mzinda wa Blantyre ukusintha. Kuona momwe mzindawu akuukongoletsera, ukhoza kuyamika. Maluwa akubzalidwa ponseponse, misewu ndi misika ikukhala yosesedwa ngakhale mwina ndi mwina zinyalala zikutsalira. Posachedwa, taonanso akunena kuti nyumba zonse zosaoneka bwino zigumulidwe. Ndipo kunena za ku Limbe, msewu wa Highway nawo ukupatsa chikoka. Koma ukafika kumalo okwerera basi zosiyanasiyana kufupi ndi msika wa Limbe, kumene ambiri amati kokwerera galimoto za kwa Manje, umakhala ngati wafikanso tauni ina, osati Blantyre. Zisakasa izi ndi malo odyera. Ofika kumene m’tauni, amalonda, ogwira ntchito ena ngakhalenso ana asukulu akati akaone kadaunda madzi amalowa mmenemo. Kudya si kudya nanga?——chimwemwe sefasi

Related Articles

Back to top button
Translate »