Chichewa

Mbuzi ndi zosavuta Kusamalira, kudyetsa

Listen to this article

Mlangizi wa ziweto wa ku G&LM Vet Services, Edwin Nyondo, wapempha alimi ambuzi kuti aziika mtima pa ulimiwu kuti azipeza phindu lochuluka.

“Alimi ambiri sapeza phindu lokwanira kaamba koti sadziwa m’mene angasamalire mbuzi zawo,” watero mlangiziyu.

Iye wati mbuzi ndi chiweto chosavuta kusamalira kaamba koti zakudya zake zimapezeka mosavuta, komanso sizivutika ndi chigodola ngati ng’ombe ndi nkhumba.

Ubwino wa ulimi wa mbuzi

Ulimi wa mbuzi ndi wophweka poyerekeza ndi wa ziweto zina

Nyondo adati ubwino wa ulimi wa mbuzi ndi wosachita kunena kaamba koti ndi ndiwo, komanso zimathandiza kuti mlimi apeze manyowa wokathira kumunda kwake.

“Munthu utha kupha mbuzi n’kupeza ndiwo zoti udye ndi banja lako. Kupatula apo, mbuzi zimapereka manyowa, komanso mkaka woti banja lako lizimwa,” watero Nyondo.

Josephy Mwasiya, mlimi wa mbuzi wa m’mudzi mwa Luniya m’dera la Mfumu Chigaru ku Blantyre, akugwirizana ndi Nyondo.

“N’zoona mbuzi ukazisamalira bwino sizichedwa kuchuluka zomwe zimachulutsa phindu la mlimi,” watero Mwasiya.

Nyondo wati mbuzi zili ndi msika waukulu m’dziko muno, komanso m’maiko akunja.

Mwachitsanzo, alimi a ku Zambia adapeza msika ku Saudi Arabia.

Malingana ndi bungwe loona za bizinesi zaulimi la Zambia Agribusiness Society (ZAS), alimi a m’dzikolo adapeza mwayi wogulitsa mbuzi zosachepera miliyoni imodzi chaka chilichonse ku Saudi Arabia.

Mitundu ya mbuzi

Nyondo wati mbuzi zilipo za mitundu yosiyanasiyna, koma alimi ambiri akuweta zachikuda zomwe zimachita bwino kwambiri ndi nyengo ya m’dziko muno.

Kupatula mbuzi zachikudazi, mlangiziyu wati pali mbuzi za chi Boer zomwe zimakula kwambiri moti mbuzi imodzi imatha kupitirira 40kg.

M’maiko ena muli mitundu ya mbuzi yochulukirirapo monga Saanen, Toggenburg, Alpine, Angola ndi Kalahari.

Malingana ndi ZAS, mtundu wa Alpine umatulutsa mkaka woposera 3.5kg patsiku.

Nyondo wati mbuzi zina zimaswa mwana m’modzi, zina awiri kapena atatu nthawi imodzi.

“N’kovuta kudziwa mbuzi zoswa oposera m’modzi pongoziona. Njira yabwino ndi kufunsa mbiri ya mbuzizo kuchokera kwa mlimi amene akugulitsa mbuzizo,” watero mlangiziyu.

Chisamaliro

Nyondo wati mbuzi monga ziweto zina zimafunika chisamaliro choyenera kuti mlimi apindule nazo.

“Mlimi akuyenera kumanga khola la m’mwamba kuti ndowe zizigwera pansi.

“Izi zimathandiza kuti mlimi asavutike kutolera ndowe zokathira kumunda; mkhola mukhale mwaukhondo ndi mouma nthawi zonse kuti mbuzi zisagwidwe ndi matenda,” watero mlangiziyu.

Iye adati mbuzi ndi zopilira ku matenda poyerekeza ndi ziweto zina, koma zimavutika kwambiri ndi nyongolotsi za m’mimba.

“Choncho mlimi ayenera kuzipatsa mankhwala a nyongolotsi zam’mimba miyezi itatu iliyonse,” watero Nyondo.

Kupatula nyongolotsi, mbuzi zimadwalanso chimfine ndi kutsegula m’mimba.

Mlimi akaona zizindikiro za matendawa azithamangira kwa alangizi a ziweto kuti amuthandize.

Nyondo, yemwe ndi mlimi wa mbuzi za chi Boer, walangiza alimi kuti azipangiratu chakudya choti adzadyetse ziweto zawo mchilimwe kaamba koti nthawiyi msipu umakhala wochepa.

Daniel Mhango, mlimi wa mbuzi wa ku Thekero m’dera la Mfumu Chikulamayembe m’boma la Rumphi, wati amazipatsa mbuzi zake madzi akumwa aukhondo, komanso salora kuti zizithithikana m’khola.

Ana a mbuzi ayenera kuyamwa mkaka wa m’maere wa mayi wawo pasanathe maola 6 kuti apeze chitetezo chokwanira m’matupi mwawo.

Kufula mphongo

Malingana ndi ZAS, kufula mphongo ndi njira imodzi yothandiza kuti mbuzi  ikhale yathanzi, yochititsa kaso, yojitcha, komanso yopanda fungo lambiri.

Related Articles

Back to top button
Translate »