Nkhani

MCP yatiphunzitsa zambiri

Listen to this article

Nkhani idali mkamwamkamwa miyezi ingapo yapitayi ndi ya msonkhano waukulu wa chipani cha MCP. Zimakaikitsa ngati kumsonkhanowo kukamangidwe mfundo zolemekeza maganizo a anthu.

Chikaiko chidakula pamene mphekesera zidali mbweee! Makamaka chipanicho chitalephera kuchititsa msonkhanowo mwezi wa April.

Chikaikocho chidakula zitamveka kuti chipanicho chikufuna kuti anthu ena, makamaka amene angobwera kumene m’chipanimo asapikisane nawo pa\mpando wa pulezidenti. Komiti yapadera ndiyo idapereka mwayi onse kuti onse amene adapereka maina awo akhoza kupikisana nawo.

Nkhani imodzi imene idatsalira idali yakuti John Tembo, amene malamulo amamuletsa kuti sangaime nawo chifukwa adaimira kale chipanichi kawiri, naye amafuna kupikisana nawo.

Koma nthumwi za kumsonkhanowo, zitafunsidwa ngati angakambirane zosintha malamulowo, zidakana kwa mtuu! Wagalu. Izi zikudza pomwe zipani zina monga cha UDF, zidasintha malamulo kuti mwana wa mtsogoleri wakale wadziko lino Bakili Muluzi, Atupele, aimire chipanichi.

Poyamba, Atupele sakadapikisana nawo chifukwa malamulo amaletsa kuti amene sadakwane zaka 35 asapikisane nawo. Nthumwi zidasintha malamulowo kuti Atupele aime.

Ndipo nthawi yosankha atsogoleri itakwana, nthumwizo zidasankha amene amaoneka ngati alendo kuposa nkhalakale za chipanicho. Izi zikungosonyeza kuti demokalase ya m’chipani yayala nthenje mu MCP.

Koma chomwe tingalangize atsogoleri a chipanichi kuti akhale okhwima mundale ndi kumulandira Kusakhale kugawanikana monga zidalili Tembo atangogonjetsa Gwanda Chakuamba mu 2003.

Related Articles

Back to top button
Translate »