Nkhani

MEC, MCP yakhutira ndi kalembera

Listen to this article

Zinthu zasintha. Anthu akulembetsa mwaunyinji m’gawo lachiwiri la kalembera wa zisankho zomwe zidzachitike m’dziko muno chaka cha mawa.

Mkulu wa bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah ndi mneneri wa Malawi Congress Party (MCP) Maurice Munthali adati ndi wokhutira ndi mmene anthu akulembetsera m’gawoli.

Ntchito ya kalembera

Izi zikusiyana kwambiri ndi momwe kalembera adayendera m’gawo loyamba momwe anthu amabwera mosisitika moti mabungwe ndi chipani chotsutsa boma cha MCP ati sadakhutire ndi momwe adayendera kalembera m’gawolo ndipo apempha MEC kuti ibwererenso m’mabomawo.

M’gawo loyamba MEC yachititsa kalembera m’maboma a Kasungu, Salima ndi Dedza pamene m’gawo lachiwiri bungweli likulembetsa anthu ku Mchinji, Nkhotakota, Dowa ndi Ntchisi.

Ansah adati MEC ndi yokhutira ndi momwe anthu akubwerera moti m’malo ena anthu odzalembetsa akumafika 700.

“Kungoyambira tsiku loyamba pa July 13 2018 anthu akubwera mwaunyinji kudzalembetsa moti m’malo ena chiwerengero cha anthu odzalembetsa chikumafika 700 patsiku,” iye adatero.

Naye mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust, Ollen Mwalubunju, watsimikiza zoti zinthu zasintha kwambiri m’gawo lachiwiri la kalembera wa zisankho.

Mwalubunju adati ngati zinthu si zisintha, 40 peresenti ya anthu ikhala atalembetsa pofika dzulo.

“Zinthu zikapitirira chonchi, ndiye kuti zolinga za demokalase zomwe n’kupereka mphamvu kwa anthu, zikwaniritsidwa,” adatero Mwalubunju.

Ngakhale anthu akupita kukalembetsa mwaunyinji, ena akubwerera osalembetsa kaamba koti zipangizo za MEC zikumaonongeka, komanso malo ena akumatsegulidwa mochedwa.

“Ngakhale zinthu zikuyenda bwino, koma nkhawa yathu ili pa makina a MEC omwe sakukhalira kuwonongeka,” adatero Munthali.

Anthu omwe adapita kwa Tembwe ndi Chiwaula ku Mchinji tsiku lotsegulira gawo lachiwiri la kalembera wa zisankho, adabwerera kaamba koti makina a bungwe loyendetsa zisankho adali atawonongeka.

M’dera la mfumu Dambe m’boma lomwelo makamaka kwa Chankhanga, Nthema, Gaandali ndi Kapiri kudali mizere italiitali ya anthu ofuna kulembetsa, koma zinthu zimayenda mwapang’onopang’ono kaamba koti makina a MEC amangowonongeka.

Ansah adati bungwe lake latumiza akatswiri m’maboma onse okhudzidwa kuti azikakonza msanga makina awo akawonongeka.

Patsiku lotsegulira kalembera ku Dowa, anthu 210 ndiwo adalembetsa kwa Kainja, 48 kwa Pheleni, 176 kwa Mbido, 126 kwa Tsache, 64 kwa Msaderera ndipo pa sukulu ya pulayimale ya Mvera padalembetsa anthu 64.

James Gama, yemwe akuyang’anira zisankho m’bomalo, adati ntchito imayenda pang’onopang’ono chifukwa amagwiritsa ntchito makina woyendera dzuwa womwe samagwira bwino ntchito chifukwa cha nyengo.

“Pano tikugwiritsa ntchito ma generator ndipo zinthu zasintha moti tikukhulupirira kuti tikwanitsa chiwerengero chomwe tikuyembekezera,” adatero Gama.

Nako ku Ntchisi ndi Nkhotakota vuto lidali kusagwira bwino ntchito kwa makina.

Malingana Summy Ng’anjo, yemwe akuyang’anira kalembera ku Ntchisi, MEC ikuyembekezera kulembetsa anthu 163 352 ndipo anthu ambiri akubwera kudzalembetsa.

Nyakwawa Galeta ya ku Nkhotakota idati m’madera ena ogwira ntchito a MEC ndi achitetezo akumabwera mochedwa.

Mlembi wamkulu wa MCP, Eisenhower Mkaka, adati momwe zinthu zikhalira m’gawo, zawonetsa poyenera kuti MEC idalephera ntchito m’gawo loyamba.

Naye mneneri wa UDF, Ken Ndanga, adati MEC isapupulume kufalitsa malipoti abodza isadafufuze mokwanira chomwe chidachitika m’gawo loyamba lakalembera.

Related Articles

Back to top button
Translate »