Nkhani

MEC yachotsa maina 13 244 m’kaundula

Listen to this article

Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lachotsa m’kaundula maina

13 244 omwe eni ake adawalembetsa kopotsera kamodzi zomwe lati n’zotsutsana ndi malamulo azitsankho.

Ansah: Amalembetsa koposa kawiri

Wapampando wa bungweli Jane Ansah ndiye adalengeza izi Lachiwiri mu mzinda

wa Lilongwe moti eni mainawo azengedwa mlandu wophwanya malamulo azisankho a dziko lino.

“Maina ena amapezeka kangapo m’kaundula ndiye tawachotsa koma eni mainawo aphwanya malamulo a chisankho a dziko lino,” watero Ansah.

Bungwe la MEC lidachita mchape wa kaundula wa za chisankho kalembera atangotha ndipo udapeza kuti chiwerengero cha anthu omwe adalembetsa kuti adzavote chaka cha mawa chakwera.

Ichi n’chifukwa chake anthu akuyenera kukatsimikiza ngati maina awo adakali m’kaundulamo.

“Anthu omwe maina awo amapezeka kangapo m’kaundula, maina enawo tafufuta

n’kusiya kumodzi ndiye mpofunika kuti anthu akatsimikize komwe adalembetserako kuti azidziwiratu komwe kuli dzina lawo,” watero Ansah.

Poyamba MEC idalengeza kuti  anthu 6 856 295 ndiwo adalembetsa m’kaundula wa zisankho za chaka cha mawa, koma litachita mchapewo, chiwerengero chatsika kufika pa 6 859 375 kutanthauza kuti poyambapo maina 3 080 adadumphidwa powerenga.

Ansah wafotokoza kuti kusinthaku kwadza chifukwa maina ena amasemphetsedwa panthawi yakalembera koma atachita mchapewo, maina onse awalondoloza.

“Maina ena amalowetsedwa molakwika m’makina, koma takonza zonse ndipo pano zonse zili bwino. Palibenso munthu amene dzina lake lingapezeke koposa kamodzi m’kaundula,” watero Ansah.

Mkulu wa bungwe lothandizira kayendetsedwe ka zisankho la Malawi

Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa wapempha kuti ayambe waona kaye lipoti la MEC asanapereke ndemanga yake, koma wati n’zodabwitsa kuti ngakhale maina ena achotsedwa m’kaundula chiwerengero cha odzaponya voti chakwera m’malo motsika.

Chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chomwe chidadandaula kwambiri ndi momwe kalembera adayendera, chati chimayembekezera kuti chiwerengero

cha anthu m’kaundula chikhoza kusintha, koma sichimayembekezera kutsintha kwakukulu ngati momwe zakhalira.

Mneneri wachipanichi Maurice Munthali wati zolakwika sizingalephele, koma adadabwa kuti chiwerengero chakwera kwambiri. n

Related Articles

Back to top button