Chichewa

Mfumu yoba mopusitsa igamulidwa mawa

Listen to this article

 

Bwalo lamilandu la majisitileti ku Ntchisi mawa likuyembekezeka kupereka chigamulo kwa mfumu ina Lachisanu idaepezeka yolakwa pamlandu wakuti inkabera anthu powanamiza.

Malinga ndi mneneri wapolisi ya Ntchisi Gladson M’bumpha, wogamula Young Ng’oma adapeza nakwawa Nyalapu (dzina lenileni Fraser Vesiyano) yolakwa pamlandu woti idapusitsa anthu ozingwa a m’mudzi mwa Chiwere kuti iwathandiza kugula feteleza ku Admarc ya m’mudzi mwake.

An artistic impression of a court room
An artistic impression of a court room

“Ng’oma adati mchitidwe wa nyakwawawo ngobwezeretsa chitukuko mmbuyo chifukwa nkuphwanya ufulu wa anthu ovutika. Chigamulo chiperekedwa Lolemba chifukwa samamva bwino m’thupi,” adatero M’bumpha Lachisanu.

Malinga ndi M’bumpha, Nyalapu, yemwe ndi wa zaka 33, adapusitsa anthu ozingwa a m’mudzi mwa Chiwere kuti awathandiza kugula feteleza ku Admarc ya m’mudzi mwake.

Iye adamata phula anthuwo kuti ali ndi njira zomwe angachite kuti athe kuwagulira fetelezayo koma pambuyo pake adayamba kuchita njomba.

“Anthuwo adali ndi makuponi koma zikuoneka kuti m’mudzi mwawo, Admarc yomwe amadalira kudalibe feteleza ndiye mfumuyo itamva idaona ngati mwayi okhupukira nkuuza anthuwo kuti iwathandiza,” adatero M’bumpha.

Iye adati mfumuyi idauza anthuwo kuti asonkhanitse makuponi komanso asonkhe ndalama zomwe zidakwana K148 500 nkumupatsa ndipo adagwirizana kuti adzabwere tsiku lotsatilalo kudzatenga fetereza wawo.

Njomba zidayamba kuwoneka anthuwo atabwera chifukwa mfumuyo idawawuza kuti abwerenso tsiku linzakero ndipo masiku amapita akuwuzidwa zomwezomwezo.

“Anthuwo atatopa adangoganiza zopita kwa mkulu wa pa Admarc yomwe imanenedwayo ndipo mkulu wa pamenepo Yasinta Jere adawauza kuti mfumuyo idagula feterezayo pa 11 January 2013,” adatero M’bumpha.

M’bumpha adati mfumu Nyalapu yomwe imachokera mdera la mfumu yayikulu Kalumo adayitsegulira mlandu wakuba pogwiritsa ntchito bodza komwe kuli kuswa ndime 278 ya malamulo a dziko lino.n

Related Articles

Back to top button