Chichewa

Milandu ya maalubino Izipita kukhothi lalikulu

Listen to this article

 

Milandu yokhudza kuphedwa kapena kusowetsedwa kwa maalubino tsopano akuti izikakambidwira mukhothi lalikulu lomwe lili ndi mphamvu yopereka chilango chokhwimirapo kuposa khothi la majisitireti lomwe chilango chomwe lingapereke n’chochepa, Msangulutso utha kuvumbula.

Milanduyi sizitengera kuchepa kapena kukula kwake pofuna kuteteza maalubino, omwe miyoyo yawo ili pachiswe kaamba ka zikhulupiriro za anthu ena zoti mafupa ndi ziwalo za anthuwa ndi zizimba za mankhwala olemeretsa.

Mneneri wa nthambi ya makhothi Mlenga Mvula wati ngakhale sadalandire kalata yotsimikiza izi, makhothi ang’onoang’ono a majisitireti ndi ovomerezedwa kusamba m’manja pankhani zotere kuti nkhothi lalikulu ligwire ntchito.

“Sindidalandire kalata iliyonse pankhani imeneyi koma kutengera momwe zinthu zilili pankhani yokhudza maalubino, mamajisireti ndi omasuka kusamba m’manja pamilandu yokhudza maalubino kuti khothi lalikulu ndilo limve ndi kupereka chigamulo ndi chilango,” adatero Mvula polankhula ndi Msangulutso Lachitatu lapitali.

Bwaloli tsopano lizizenga milandu yokhudza maalubino
Bwaloli tsopano lizizenga milandu yokhudza maalubino

Iye adati m’ndondomeko za makhothi, khothi lililonse lili ndi mlingo womwe silingabzole popereka chilango ndiye potsatira madandaulo a anthu kuti kuzunza maalubino kukunka mtsogolo kaamba ka zilango zochepa, n’kofunika kuti khothi lalikulu ndilo lizizenga milanduyi.

“Majisitireti sangapitirire mlingo wina wake popereka chilango, ndiye kutengera zilango zomwe anthu akufuna kuti ozunza maalubino azilandira, majisitireti akuyenera kutumiza mlanduwo kukhothilalikulu,” adatero Mvula.

Chitsanzo cha nkhaniyi chapezeka ku Mchinji komwe majisireti Rodwell Mejja Phiri wasamba m’manja pamlandu wa Zione Gabina Kamngola, wa zaka 25, yemwe akuzengedwa mlandu womuganizira kuopseza msuweni wake, Gertrude Ulaya, wa zaka 22, yemwe ndi wachialubino.

Mneneri wa polisi ku Mchinji, Moses Nyirenda, wati Kamngola akumuganizira kuti adanena msuweni wakeyo kuti iye ndi ndalama ndipo akadakhala mwana wake akadamupha. Nkhaniyi akuti idaopsa msuweni wakeyo ndi mayi ake, Mary Ulaya, omwe adakadandaula kupolisi.

Iye adati apolisi atafufuza za nkhaniyi, adatsegulira Kamngola mlandu woopseza munthu ndi mchitidwe womwe ungayambitse chisokonezo.

Malinga ndi Nyirenda, majisitireti Mejja Phiri adanena kuti nkhaniyo idamukulira malingana ndi mlingo wa chilango chomwe angapereke ndipo mmalo mwake adapereka kalata ya limandi ndipo mayiyo ali ku Maula kuyembekezera kukaonekera kukhothi lalikulu ku Lilongwe.

Titamufunsa ngati sikumulakwira wozengedwa mlandu waung’ono ngati uwu kumutumiza kubwalo lalikulu mlandu wake usanazengedwe kubwalo la majisitireti, Mvula adati pakhothi lililonse, munthu amalandira chilungamo mofanana chifukwa mbali zonse ziwiri zokhudzidwa zimakhala ndi mpata wonena mbali zawo ndipo chigamulo chimachokera pa zokamba zawozo.

“Zilibe kuti ndi khothi la majisitireti, khothi lalikulu kapena la Supreme, ayi. Kulikonse mbali zokhudzidwa zimapatsidwa mpata wonena mbali zawo ndipo chigamulo chimachokera pamenepo,” adatero Mlenga.

Iye adatsindika kuti nkhani yaikulu yagona pokhwimitsa chitetezo cha maalubino kuti anthu akaona zilango zikuluzikulu zomwe zikuperekedwa ayambe kukhala ndi mantha ndipo mchitidwe wozunza maalubino uthe.

Potsirapo ndemanga, katswiri wa zamalamulo kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Edge Kanyongolo, adavomereza kuti mlandu wotere ndi mlandu waung’ono woyenera khothi la majisireti, koma zikutengera mfundo zomwe iye wagwiritsa ntchito posamba m’manja.

“Umenewu ndi umodzi mwa milandu ing’onoing’ono potengera malamulo ogamulira milandu ndipo umayenera kugamulidwa ndi majisireti chifukwa chilango chake nchochepa. Ngakhale zili chonchi, zimatengera kuti iye wawonaponji pankhaniyo chifukwa pazifukwa zina akhoza kuutumiza kukhothi lalikulu,” adatero Kanyongolo.

Naye mlembi wa bungwe la maloya Khumbo Soko adagwirizana ndi kanyongolo ponena kuti majisitireti aliyense ali ndi mpata wofunsa chiunikiro cha khothi lalikulu ngati akuona kuti nkhaniyo ikuposa mphamvu zake.

Posamba m’manja pa mlanduwo pa 3 June, 2016, Mejja Phiri adati adauzidwa kuti milandu yonse yamtunduwu aziitumiza kukhothi lalikulu kuti anthu opezeka olakwa azilandira chilango chokwanira.

Gawo 88 (1) la milandu ndi zilango zake yokhudza mlandu woopseza munthu ili ndi magawo awiri omwe kaperekedwe ka chilango chake n’kosiyana.

“Mlandu woopseza womwewu, munthu akhoza kumangidwa mpakana moyo wake wonse ngati adatchulapo za kupha, pomwe ngati adangoti ndikumenya poopsezapo, chilango chachikulu chomwe angalandire ndi zaka zitatu kundende,” adatero Nyirenda.

Iye adati chokhacho chotchula kupha ndi kutengera kuti woganiziridwayo adaopseza munthu wa mtundu womwe dziko lonse lapansi likudandaula kuti uli pachiwopsezo chachikulu ndi mlandu waukulu.

Kamngola ndi msuweni wakeyo onse amachokera m’mudzi mwa Tembwe, kwa mfumu Mlonyeni m’boma la Mchinji. n

Related Articles

Back to top button
Translate »