Chichewa

Minibasi zikwera Mwachinunu

Listen to this article

 

Nthawi zonse minibasi zikamakweza mtengo, makamaka mafuta akakwera, bungwe la eni minibasi limalengeza, ndi kuika mitengo ya minibasi kuti aliyense adziwe. Koma kuchokera Loweruka lapitalo, mitengo ya minibasi m’madera ena idakwera mwachinunu.

Izi zidachitika patangotha tsiku limodzi kuchokera pomwe oyendetsa minibasi adanyanyala ntchito zawo ati pokwiya ndi zilango zina zimene amalandira akaphwanya malamulo a pamsewu.

Amalawi amene tacheza nawo ku Blantyre, Lilongwe ndi Mzuzu adati ndiokhudzidwa ndi kukwezaku, komwe cholinga chake sichikumveka.

Mandiya: Okwera akuyenera kupereka
yochuluka basi

Mmodzi mwa anthu omwe akhudzidwa ndi mitengoyi, Sydney Ching’amba wa ku Chilomoni yemwe amagwira ntchito ku Ginnery Corner mumzinda wa Blantyre, wati ichi ndi chitonzo ndipo okwera akuyenera kuchitapo kanthu kuti mitengo ibwerere.

Kafukufuku wa Msangulutso wapeza kuti mitengoyi yakwera ndi K50 kapena K100 m’madera osiyanasiyana m’mizindayo.

Malingana ndi mmodzi mwa madalaivalawa mu Limbe, Fatchi Madani, iyi ndi njira yoti galimoto itulutse ndalama zomwe eni minibasi amafuna patsiku ngakhale pali malamulo okhwimawa.

“Okwera akuyenera kupereka ndalama yochuluka basi. Patsiku bwana amafuna K10 000 ndipo kutenga atatu pampando pa K500 kukawasiya kwa Goliati ndi phada ameneyo. Ngakhale tisatenge anayi-anayi pampando ndalama izipezeka yokwanira chifukwa cha mitengoyi,” adatero Madani.

Naye Phillip Bwanali, woyendetsa galimoto pakati pa Limbe ndi Blantyre, adati akweza mitengo chifukwa sakuloledwa kunyamula katundu [chimanga, mtedza ndi zina] yemwe okwera amamulipira mwa padera.

“Tatero kuti tisavutike ndi kupewa ena kuyamba kuba ndi umbanda. Mmene chilili chuma cha dziko lino anthu ambiri sangakwanitse kutenga katundu pa matola omwe ndi okwera mtengo kusiyana ndi maminibasi,” iye adatero.

Poyankhapo, mkulu wa bungwe la eni minibasi la Minibus Owners Association of Malawi (Moam), Coaxley Kamange adati ndi odabwa ndi zimenezi ndipo wangomva mphekesera kuti madalaivala achita moteremu.

“Izi sizikutikhudza. Aliyense akhoza kuchita chili chonse ndi mitengo chifukwa lamulo likulola anthu kutero. Takhala tikudzudzulidwa ndi bungwe la Competition and Fair Trading Commission (CFTC) pamene timakonza mitengo mmbuyomu ndipo tidasiya,” adatero Kamange.

Iye adati izi ndi zosokoneza anthu chifukwa akudziwa zakusinthaku ali m’minibasi kapena padepoti.

“Timayenera kutenga gawo pa chiganizochi kuphatikizapo okwera kuti mitengo ikhale yokomera onse. Bungweli [CFTC] lidati tisamakonze mitengo ya minibasi, koma padakalipano ndondomeko yabwino palibe,” adatero Kamange.

Mkulu wa bungwe loona ufulu wa okwera la Passengers Welfare Association of Malawi (Pawa), Don Napuwa, adati izi ndi zokhumudwitsa ndipo madalaivala sakuyenera kukweza mitengo ya galimoto chifukwa boma langokhwimitsa ndi kuyamba kutsatsa malamulo omwe adalipo kale.

“Madalaivala akusokoneza. Ngakhale kunyanyala ntchito komwe adachita sabata yatha eni galimoto sadadziwitsidwe. Mitengoyi imakwera potengera mtengo wa mafuta ndipo mafuta sanakwere. Oyendetsawa alibe danga lokweza mitengo,” adatero Napuwa.

Iye adapempha okwera maminibasi kukana mitengoyi pokakamiza madalaivala ndi makondakitala kuwatenga pa mitengo yakale. n

Related Articles

Back to top button