Chichewa

Minibasi zivuta pa Wenela

Listen to this article

 

Si kuti ndikamba za kutentha kwa pa Wenela. Si kuti ndinena za kukwera mtengo kwa zinthu. Si kuti ndinena za chipasupasu chagundikanso ku Ukafuna Dilu Fatsa. Ayi, sindinena zonsezo.

Si kuti ndibwereza kunena nkhani ya othawa nkhondo uja Adona Hilida. Pajatu wamisala adaona nkhondo, ngakhale adali kulota chabe.

art

Inde, ngati mumayembekezera kuti ndinena za amisala ena amene akunena zamisala kuti kusiyana pakati pa osauka ndi olemela kusakhale kwakukulu mwalemba m’madzi. Abale anzanga, izi zingatheke pa Wenela pano?

Zingatheke bwanji osauka ndi olemera kukhala osasiyana kwambiri? Zingatheke bwanji pamene ana a anthu olemera akuphunzira sukulu zodula pomwe ana a amphawi akuphunzira pansi pa mtengo ngakhale mvula ikugwa?

Sindinenanso kuti nzosatheka, zili ngati ngamira kuyesera kulowa pabowo la singano. Zitheka bwanji pomwe osauka akupatsidwa Panado pomwe akudwala malungo chonsecho olemera olamula ndi otsutsa akutumiza ana awo kuzipatala za ku Soweto?

Misala! Zosatheka! Za ziiii! Zopanda ndi kamchere olo kamodzi!

Pa Wenela tsikulo padavuta. Kudali chifwirimbwiti. Nkhani idavuta ndi ya minibasi. Nthawiyo nkuti apolisi atagwira minibasi zosachepera 70.

Chifukwa?

Ati timatenga mafolofolo. Kodi okwera timawakakamiza kukwera folofolo? Ndimayesa iwowo amapanikizana ngati nsomba zam’chitini chifukwa amakhala pachangu?

Kodi okwera sadziwa kuti tikaloza chala pansi ndiye kuti tikufunsa ngati kutsogolo kuli boma? Kodi sadziwa kuti tikazindikira kuti kuli boma, mmodzi kapena awiri amene anachititsa kuti ilakwe atsika?

Kodi iwowo sadziwa kuti ngati yalakwa ndi mmodzi kondakitala akhoza kutsika nkuuza mzibambo mmodzi agwire chitseko ngati kondakitala, iye nkuthamanga kudutsa boma? Simudaonepo woyendetsa akuuza wokwera mpando wakutsogolo kuti akhalire lamba poopa boma? Mudaona wokwerayo akukana?

Ndiye kudali kuotcha mateyala.

“Mutibwezere mabasi athu! Mugwira bwanji mabasi, mukufuna tikadye kuti?” adali kuimba chotero makondakitala, madalaivala, ife oitanira komanso ena okwera.

Ndiye mwati umphawi ungathe?

Gwira bango! Upita ndi madzi! n

Related Articles

Back to top button