Nkhani

Mipingo yakonzeka zophunzitsa anthu za katemera wa Covid 19

Listen to this article

Thunthu loyamba la katemera wa Covid 19 lidafika mziko muno sabata ikuthayi ndipo malingana ndi mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera, magulu oyambilira akhala akulandira katemerayo posachedwa.

Muuthenga wake Lamulungu lapitali, Chakwera adati majekeseni opelekera katemerayo adali kale m’dziko muno ndipo katemera weniweniyo amayembekezeka dzulo Lachisanu cha m’ma 4 koloko.

Mneneri wa unduna wa zaumoyo Joshua Malango Lachinayi adatsimikiza kuti katemerayo afika Lachisanu

Chakwera adati boma likuyesetsa kulimbana ndi matenda a Covid 19 kuti chiwerengero cha anthu opezeka ndi matendawo chiitsike kufika pa anthu 5 mwa 100 aliwonse kapenanso kutsikirapo.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe adayamikira ganizo la katemerayo koma adati mpofunika kuchilimika kuphunzitsa anthu kuti adziwe zoona za katemerayo.

“N’zofunika kumakhala tcheru chonchi,  tathanako ndi miliri ina mmbuyomu ndi katemera koma chofunika n’kuphunzitsa anthu kuti amvetsetse za katemerayo apo ayi akhoza kuvuta kaperekedwe kake,” adatero Jobe.

Malingana ndi kalata yochokera kuunduna wa zaumoyo, ogwira ntchito zachipatala ndi magulu ena omwe ali ndi mavuto a zaumoyo m’matupi mwawo ndiwo adzayambe kulandira katemerayo.

“Monga tikudziwa zachiopsezo chomwe anzathu a zaumoyo ali nacho, katemera oyambilira adzalandira ndi iwowo limodzi ndi anthu omwe ali ndi mavuto azaumoyo mmatupi mwawo kuti atetezedwe,” idatero kalata yaundunawo.

Pakatipo kwakhala kukumveka manong’onong’o okhudza katemerayo koma unduna wazaumoyo udatsutsa manong’onong’owo ndi kupempha magulu osiyanasiyana monga mipingo kuti ithandize pophunzitsa anthu zaubwino wa katemerayo.

Kudzera m’mabungwe monga Malawi Interfaith Aids Association (MIAA) atsogoleri a mipingo akhala akukumana ndi kukambirana za gawo lomwe angatengepo pa nkhondo yolimbana ndi corona.

Wapampando wa bungwe la MIAA Gilford Matonga adati atsogoleri a mipingo ndi okonzeka tsopano kuphunzitsa anthu za katemerayo koma adati mpofunika kuti atsogoleri onse akhale ndi uthenga umodzi.

“Sizingaphule kanthu kuti mpingo uliwonse ukhale ndi uthenga wake wake  ayi, tikufunika tonse tinyamule uthenga umodzi ndi kuuza anthu zoona ndipo takonzeka kutero,” adatero Matonga.

Jobe adati mpofunika kusiyira ntchito yopanga mauthengawo akadaulo enieni odziwa za mankhwala kuti uthenga omwe uzipita kwa anthu ukhaledi ochokera pa nzeru zaukadaulo.

“Nkhaniyi kuti ithe bwino, boma lisiyile akadaulo odziwa za mankhwala mu unduna wa zaumoyo kuti ndiwo apange mauthenga ndi kufalitsa malingana ndi ukadaulo wawo. Boma lionetsetse kuti magulu ena ngati andale asakhale patsogolo ndi nkhaniyi,” adatero Jobe.

Iye adati Amalawi akuyenera kutenga katemerayu ngati momwe amatengera katemera wina aliyense akafika ndi kutsogoza chikhulupiliro kuti zonse ziyende bwino.

“Katemera sasiyana kwambiri ndi mankhwala. Mkati mothandizika, ena amatha kukumanabe ndi zovuta zina koma zimakhala zopepuka kusiyana ndi vuto lomwe athana nalolo. Tikufuna zimenezi anthu auzidwiretu ngati zilipo,” adatero Jobe.

Iye adati si bwino kulekelera munthu afe ndi nthenda yoti ili ndi katemera kotero nkofunika uthenga okwanira kuti anthu amvetsetse zowona zake za katemerayu ndi kumulandira ndi manja awiri.

Ngakhale izi zikuchitika, mayiko ena makamaka olemera akangalika kugula katemerayo kusonyeza kuti mmayikomo amuvomereza.

Posachedwapa, Pulezidenti wa dziko la South Africa Cyril Ramaphosa komanso nthumwi ya maiko aazungu (EU) Ivo Hoefkens adadzudzula maiko olemera omwe akugula mankhwala oposa omwe akufuna m’dziko mwawo ponena kuti apereka chiopsezo ku maiko osauka.

Related Articles

Back to top button
Translate »