Nkhani

Mitsinje isefukiranso chaka chino—azanyengo

Listen to this article

Nthambi yopima zanyengo ya mdziko muno ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati chaka chino kukhala kusefukira kwa madzi, maka kuchigawo cha Kummwera.

Izi zalankhulidwa sabata yatha pamene nthambiyi idaitanitsa atolankhani kuwafotokozera momwe nyengo ya mvula iyendere chaka chino.floods

Nthambiyi yati pamene madera ena asowe mvula, madera okwera alandira mvula yoopsa yomwe ingachititse kuti kukhale kusefukira kwa madzi.

Zopeza za nthambiyi, zikuonetsa kuti mwayi ndi waukulu kuti madera ambiri alandira mvula yoposera mlingo wake pamene ena alandira mvula ya mlingo wake ndi ena kusoweratu mvulayi.

Nthambiyi yati pakati pa October ndi December, chigawo cha Kumpoto chili ndi mwayi waukulu wolandira mvula yabwino. Umu ndi momwenso zilili kuchigawo cha Kummwera koma mwayi wolandira mvula yambiri ndi wochuluka.

Zoloserazi zikuti miyezi ya January ndi March, zigawo ziwirizi zidzalandira mvula yambiri, zomwe zikusonyezeratu kuti kusefukira kwa madzi chaka chino ndi nkhani yosayamba.

Mneneri wa DCCMS, Ellina Kululanga, akuti nkhani ya kusefukira kwa madzi isachotsedwe chifukwa miyezi ya January ndi March ndiyo ikuopsa ndipo anthu akonzekere.

“Mbali yaikulu ya dziko lino ikuonetsa kuti ilandira mvula ya mlingo wake komanso kuposera apo,” adatero.

Chaka chatha mpaka kumayambiriro a chaka chino, ngakhale madera ambiri mvula sidagwe yokwanira, madzi osefulira adavuta kwina ndi kwina maka zigawo za Kumpoto (Mzuzu) komanso maboma a Chikwawa, Nsanje ndi Mulanje komwe anthu ena adataya miyoyo yawo komanso ziweto, nyumba ndi katundu zidakokoloka.

Tikukamba pano anthu oposa 16 000 akukhalabe azingwa pachilumba china ku Makhanga m’boma la Nsanje pomwe akudikira boma kuti liwasamutse. n

Related Articles

Back to top button
Translate »