Nkhani

Miyezi inayi idutsa mafumu osalandira mswahala

Listen to this article

Nyakwawa komanso magulupu akudandaula kuti matumba awo abooka kaamba koti patha miyezi inayi asakulandira mswahala.

T/A Nthache wa ku Mwanza wati kusalandira mswahalaku kwakhudza ntchito zachitukuko kumeneko chifukwa mafumuwa sakutumiza anthu kuti akagwire ntchito zachitukuko monga kulambula misewu ndi zina.

“Mafumuwa adzandidandaulira. Ndikawaitana kuti tikagwire ntchitozi zikuvuta, sakutumiza anthu awo zomwe zikuchedwetsa ntchito zambiri zaachitukuko,” adatero Nthache.

Koma nduna ya za maboma aang’ono, Grace Maseko, wati izi sakudzidziwa chifukwa mafumu onse adalandira ndalama zonse zomwe zidatsala mu December chaka chatha.

“Ngati pali ndalama zomwe sizidaperekedwe ndi za mwezi wa March basi,” adatero Maseko.

Iye adatinso boma lidasintha momwe mafumuwa angalandirire ndalama zawo. “Poyamba timawaikira kubanki koma pano amalandira pamanja pa 27 mwezi ulionse,” adatero Maseko.

Koma malinga ndi mafumuwa, zomwe akunena Maseko ndi njerengo.

Nyakwawa Mussa ya kwa STA Amidu kwa T/A Kalembo m’boma la Balaka akuti kumeneko akhala akufunsa kwa omwe amabweretsa malipiro awo koma palibe amalongosola chomwe chikuchitika.

“Sizili bwino, ngakhale malipiro athu ndi ochepa, tikuyenera kulandira,” adatero Mussa.

Gulupu Kapochi wa kwa T/A Zilakoma m’boma la Nkhata Bay wati kumenekonso malipirowa sadalandire kwa miyezi inayi.

“Ntchito zachitukuko tayimika kaye kuti tifufuze za malipiro athu. Tidakagwada kwa gogocharo koma nawonso akuti sakudziwa zomwe zikuchititsa kuti tisamalandire malipiro athu. Tikupempha boma litithandize,” adatero Kapochi.

Mafumu enanso a ku Balaka ndi Ntcheu omwe adati tisawatchule maina, adatsimikiza za nkhaniyi ndipo ati palibe chifukwa chomalimbikira ntchito zakumudzi chikhalirecho sakulandira malipiro awo.

Muulamuliro wa DPP, malemu Bingu wa Mutharika adati mafumuwa azikalandirira ndalama kubanki kuti afanane ndi ogwira ntchito m’boma.

Izi zidasinthadi. Mafumu adayamba kulandirira malipirowo kubanki kusiya njira yomakalandirira kwa DC. Njirayi mafumuwa, maka magulupu ndi nyakwawa, adaidandaula ponena kuti akuyenda mtunda wautali koma kukatenga malipiro ochepa. Iwo adati malipirowo akungothera kukwerera basi kapena matola.

Chaka chatha mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda, adalamula kuti mafumuwa ayambenso kulandira pamanja. Chisinthireni, mafumuwa akhala akudandaula kuti malipiro akumachedwa.

Padakalipano, magulupu akulandira K5 000 pomwe nyakwawa ndi K2 500 pamwezi.

Mafumu ena akhala akudandaula kuti malipirowa akuchepa ndipo boma liwaonjezere chifukwa zinthu zakwera kutsatira kugwa kwa ndalama ya kwacha.

Ogwira ntchito m’boma ndi ena adakwezeredwa malipiro awo koma mafumuwa sadaone kusintha.

Related Articles

Back to top button