Chichewa

‘Miyoyo ya Amalawi ili pachiopsezo’

Listen to this article

Mkulu wa bungwe loona za umoyo la Malawi Health Equity Network (MHEN) Martha Kwataine wati nzomvetsa chisoni kuti dziko la Malawi lasemphanitsa zoyenera kuika patsogolo. Iye wati izi zaika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo.

Kwataine adanena izi kaamba ka ganizo la boma losiya kulemba ntchito madokotala 51 omwe amaliza maphunziro awo kusukulu ya ukachenjede ya College of Medicine ati popeza bomalo silikulembanso anthu ntchito.

Koma unduna wa zaumoyo wati wasintha maganizo ake ndipo tsopano ulemba ntchito madokotalawa ngakhale kumene kuchokere ndalama zowalipira sikukudziwika.

kwataine_martha

Polankhulana ndi Tamvani mkati mwa sabatayi, Kwataine adati n’zachisoni kuti boma lafika pokanika kulemba ntchito adotolo panthawi yomwe dziko lino likulira chifukwa chakuchepa kwa madotolo m’zipatala.

Iye adati n’zodabwitsa kuti boma lomwe lakhala likudandaula kuti madokotala akuthawa m’dziko muno kutsatira ntchino zonona kunja, pano likukana kuwalemba ntchito.

“Nanga akatithawa, kapena anthu akasiya kupita kusukulu ya udotolo, titani?” adadabwa Kwataine.

Iye adati n’zachisoni kuti ganizo la boma posalemba ntchito madotokotalawa kuika miyoyo ya Amalawi ambiri pachiospezo chifukwa madokotala alipo kale ochepa.

“Ndikulankhula pano zinthu sizili bwino m’zipatala zambiri momwe anthu akumwalira ndi matenda ochizika kaamba kakuchepa kwa madotolo,” Kwataine adatero.

Ndipo m’sabatayi madokotala onse m’dziko muno adaopseza kuti anyanyala ntchito ngati boma sililemba ntchito anzawowo pakutha pa sabata ziwiri.

Koma pozindikira kuti zinthu sizikhala bwino madokotalawo akanyanyala ntchito, unduna wa zaumoyo ndi a kuunduna wa zachuma adakhala pansi n’kugwirizana kuti madokotalawo alembedwe ntchito zisanafike poipa.

Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe adatsimikiza za nkhaniyi Lachinayi polankhula ndi mtolankhani wa The Nation, koma adati undunawo sukudziwa kuti ndalama zolipira madokotala atsopanowo zichokera kuti.

Naye mneneri wa unduna wa zachuma Nations Msowoya adati ngakhale adagwirizana zoti madokotalawo ndi anamwino alembedwe ntchito, sakudziwa kuti malipiro awo azitenga kuti.

Malinga ndi kalata yomwe adatulutsa a bungwe la Medical Doctors Union of Malawi mogwirizana ndi bungwe la Society of Medical Doctors, kulemba ntchito adotolowa kuthandiza kuchepetsa kuperewera kwawo m’zipatala.

Kalatayo idati boma la Malawi liganizire za umoyo wa anthu m’dziko muno womwe ukufunika kuikidwa patsogolo ndipo zina zonse zibwere pambuyo.n

Related Articles

Back to top button