ChichewaEditors Pick

Mkangano uimitsa kumanga sukulu

Listen to this article

 

Njovu zikamamenyana umavutika ndi udzu, adatero akulu a mvula zakaale. Izi zapherezeka ntchito yomanga sukulu ya sekondale yoyendera ku Chombe m’boma la Nkhata Bay itaima kwa zaka zisanu kaamba ka mkangano wa malo womwe unabuka m’deralo pakati pa Gulupu Malepa ndi mwini munda womwe akufuna kumangapo sukuluyo, Michael Mkandawire.

Pomwe deralo lili ndi sukulu za pulaimale 11, lilibe sukulu ya sekondale, zomwe zikukweza chiwerengero cha ana osiyira sukulu panjira.

Anthu a m’deralo ataona vutoli adapempha kuboma sukulu ya sekondale m’chaka cha 2010. Motsogozedwa ndi mfumu yawo, Gulupu Malepa, adapeza malo pomwe adaumbapo njerwa kuti ntchitoyi iyambike.

Sichinga: Tili okonzeka  kusamutsa njerwa
Sichinga: Tili okonzeka
kusamutsa njerwa

Koma zinthu zidasokonekera pomwe zidadziwika kuti malo adaperekedwawo, udali munda wa Mkandawire, yemwe panthawiyo adali ku Dar es Salaam m’dziko la Tanzania.

Mkandawire adauza Msangulutso kuti mchemwali wake ndiye adamuimbira foni kumudziwitsa kuti munda wake ukupita.

Iye adati izi zidachititsa abwerere kumudzi komwe adadzapeza  zinthu zitavuta.

“Ndidapempha kuti ngati akundilanda malowa, andipatse ena zomwe sizidatheke, koma chonsecho malowa ndi oti adatisiyira ndi agogo athu.

Pano akuti ndizipita kwathu ku Rumphi komwe sindikukudziwa chifukwa ndinabadwira konkuno m’chaka cha 1972, nawo mayi anga adabadwiranso kuno m’chaka cha 1950,” adatero Mkandawire.

Iye adati chaka chino pamalopo sadalimepo chifukwa choospezedwa kuti atidzimulidwa.

“Amfumu akufuna chitukuko chikhale pakhomo pawo, chifukwa akufuna adzakokenso magetsi sukuluyi ikadzabwera ndipo malo okhawo omwe apezeka ndi munda wanga,” iye adatero.

A komiti ya chitukuko cha m’mudzi village development committee (VDC) ya Malepa ataona mpungwepungwewu  adapeza malo ena, koma mfumuyi ikukanitsitsa kuti sukuluyi ikamangidwe malo ena.

Malinga ndi wapampando wa komitiyi, Jefferson Sichinga, malo ena apezeka m’dera la mfumu Malenga ndipo ndi okonzeka kusamutsirako njerwa zomwe zidaotchedwa pamalo akalewo.

“Vuto ndi loti pachiyambi a gulupu adatisonyeza malo a mwini; nthawi yoti tiyambe chitukuko itakwana mwini wake adatulukira ndipo ngakhale tidagwirizana kuti timangapo timangoyenera kusuntha chifukwa mpamunda wa chinangwa wa mwini wake,” adatero Sichinga.

Mkandawire: Akuti ndizipita  kwathu
Mkandawire: Akuti ndizipita
kwathu

Iye adati vuto lalikulu lomwe lilipo ndi loti Malepa akufuna chitukuko m’khonde mwake.

Malepa adavomereza zoti akufunadi chitukukocho chipite dera lake kaamba ka magetsi.

“Eya. Zoonadi chifukwa ndine mfumu ya chitukuko,” adalongosola Malepa. Iye adaonjezera kuti Sichinga yemwe ndi wapampando wa VDC akufunanso kuti malo a sukuluwo asinthe kaamba koti adasowetsa uvuni wa njerwa zokwana 100 000 ndipo akuthawa, nkhani yomwe Sichinga akuikana.

Polankhula naye pafoni Lachitatuli, Malepa adatemetsa nkhwangwa pamwala ponena kuti chitukukochi sichisuntha kaamba koti malo adaperekawa ali pakati pa derali.

“Ine ndi a T/A Timbiri tikufuna sukulu ikhale pamalo omwe tidapereka m’chaka cha 2010 pa Chombe Zion. Khansala wa dera lino Menson Simkonda ndiye akufuna kusuntha sukulu kuti ikhale kwawo ndi cholinga chodzawina mavoti mu 2019,” adatero Malepa.

Iye adaloza zala khansalayo komanso wapampando wa VDC kuti ndiwo akumunyenga Mkandawire kuti akanize malowo.

“Si malo a Mkandawire, koma akhansala ndi omwe akumpangitsa ndipo palowa ndale, pakufunika aboma komanso a Timbiri abwere tidzakhale pansi,” adalongosola Malepa.

Iye adati sadalande Mkandawire malo.

“Ngati ali malo ake apite kubwalo la milandu. Akadatisiyira malowo pano tikanakhala titamanga kale sukulu ndipo ana akuphunzirapo. Ine sindingalole ana azivutika kusowa sukulu chifukwa cha malo,” idatero mfumuyo.

Koma khansala wa Mpamba Ward, Simkonda adati chomwe anthuwo akufuna ndi chitukuko.

“Amfumu akufuna malo a munthu pomwe anthu aperekanso malo ena. Mfumu imodzi singapweteketse ana,” adatero Simkonda.

Ndipo malinga ndi wampando wa VDC, katundu wa ndalama zokwana K12 miliyoni woti amangire buloko imodzi adabwerera masiku apitawa chifukwa aboma atafika kumalowo sadapeze malo oti n’kusunga katunduyo.

Limodzi mwa mabungwe omwe akugwira ntchito m’deralo kuchokera ku mpingo wa CCAP mu Sinodi ya Livingstonia, m’thambi yake yoyang’ana za chitukuko ndi maufulu osiyanasiyana ya Church and Society, yati m’derali mukufunika sukulu mwachangu.

Mmodzi mwa oyan’ganira pulojecti yomwe cholinga chake ndi kupereka mphamvu kwa anthu pa zitukuko pokweza ulamulilo wa ma boma ang’ono Robert Ndovi adati zivute zitani, pofika September ana a fomu 1 akhale atayamba kuphunzira.

“Ana ndi omwe akuluza chifukwa cha mkanganowu; anthu a dera lino angopeza nyumba zomwe zilipo kale kuti chaka chino maphunziro ayambe,” adatero Ndovi.

Polankhulapo mkulu woona maphunziro m’bomali Mzondi Moyo adati ofesi yake ikudziwa za kuchedwa kwa ntchito yomanga sukuluyi kaamba ka nkhani ya malo.

“Mwini malowa adadandaula kuti ndi pokhapo pomwe amadalira ndi banja lake, ndipo malowo akatengedwa avutika,” adatero Moyo.

Iye adati masiku apitawa adakumana ndi DC wa bomali, Alex Mdooko, komanso wampando wa komiti ya khonsolo ya bomalo, Hastings Mkandawire, pa zatsogolo la ntchitoyi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »