Nkhani

Mkokemkoke patsiku la chisankho

Listen to this article

Zipani zotsutsa boma zalembera bwalo la milandu la Supreme Court kuti lifotokoze bwino pa za yemwe akuyenera kusankha tsiku loti Amalawi adzasankhe mtsogoleri wa dziko lino.

Izi zikudza pomwe mpaka lero zikuoneka kuti tsiku lenileni silinakhazikike kuchokera pomwe bwalo la Constitutional Court lidalengeza kuti chisankhocho chichitikenso pasanathe masiku 150 kuchokera pa 3 February.

Msukwa: Tiadasankha June 23

Kuchokera apo, aphungu a Nyumba ya Malamulo adasankha kuti chisankhocho chichitike pa 19 May koma mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adakana kusainira biloyo. Apa bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza kuti likukonza zoti chisankhocho chidzachitike pa 2 July, patangotsala tsiku limodzi kuti masiku 150 akwane.

Koma Lachinayi, komiti ya Nyumba ya Malamulo younikira za malamulo idakumana ndi wapampando wa MEC Jane Ansah komanso mlangizi wa boma pamilandu Kalekeni Kaphale adagwirizana kuti chisankhocho chidzakhaleko pa 23 June.

Potsatira izi, woimira zipani zotsutsa dzulo adakapempha  bwalo la Supreme Court kuti litambasule bwino yemwe akuyenera kusankha tsiku lochititsa chisankhocho.

Woimira mtsogoleri wa UTM Party Khumbo Bonzoe Soko adati adakamang’ala kubwalolo lomwe lidavomerezana ndi bwalo la Constitutional Court kuti chisankho cha chaka chatha sichinayende bwino ndipo china chichitikenso.

“Pounikira bwino chigamulo cha Supreme Court komanso poona za malamulo a chisankho, sizikumveka bwino ngati woyenera kusankha tsiku latsopano ndi a MEC kapena Nyumba ya Malamulo.”

Polankhula atakambirana ndi Kaphale komanso Ansah, wapampando wa komitiyo Kezzie Msukwa adati adamvana kuti chisankho chikhalepo pa 23 June.

“ Tinawafunsa a MEC ndipo atitsimikizira kuti zokonzekera zili mmalo mwake moti chomwe chatsala n’kusandutsa tsikuli lamulo basi,” adatero Msukwa.

Malinga ndi Kaphale, ntchito yake patsikulo idali kuunikira mwina  ndi mwina tsikulo lisanasankhidwe.

“Ntchito yanga idali kungounikira basi osati kupanga tsiku ndiye ndaunikira mofunikiramo. Chofunika kwambiri chomwe ndawauza n’kutsata zomwe malamulo a dziko lonse okhudza chisankho chovomerezeka amanena,” adatero Kaphale.

Pankhani yoti makomishona ena ntchito ikutha pa 5 June 2020, Msukwa adati si ntchito ya komitiyo kukambirana poti Mutharika akudziwa kale zonsezo komanso akudziwa choyenera kuchita.

“Ntchito yathu idali kupanga tsiku ndipo tapanga zinazo ndi udindo wa mtsogoleri wa dziko lino. Komanso ku MEC kuli likulu ndikukhulupirira kuti akudziwa chochita kuti chisankho chidzapitirire ngakhale ntchito ya makomishona itatha,” adatero Msukwa.

Related Articles

Back to top button
Translate »