Chichewa

Mlaliki wozizwitsa pa Wenela

 

Tsikulo pa Wenela padali mapemphero. Abale anzanga kwadzatu alaliki. Koma ine sindiiwala ntchito za ulaliki za Shadreck Wame amene adatipezapo kwathu kuja kwa Kanduku.

Iyetu palibe tsiku ndi limodzi lomwe limene adayesera kusandutsa miyala kukhala masikono. Palibe tsiku ngakhale limodzi limene adayerekeza kunena kuti akhoza kuchita zozizwitsa posandutsa atate wawo kukhala mayi wawo.

Ndikumbuka ulaliki wa mlaliki wa ku Mdikayo pomwe adafika kwathu kwa Kanduku. Adalumikiza malembo oyera ndi nthano yake.

art

“Padali fisi yemwe adaona mayi wina akuyenda atasenza dengu lake. Mayiyo amati akamayenda, amagwedeza mkono wake. Fisi adayamba kutsatira mayiyo poganiza kuti m’dengu mudali nyama yochuluka. Ndipo poona mkonowo ukuyenda kupita kutsogolo, kumbuyo, kutsogolo, kumbuyo, fisi adali kutsatira.

“Mumtima adali kunena ‘igwa n’tola’. Mayi adaoloka mitsinje, fisi pambuyo amvekere: ‘igwa n’tola’. Mayi adatsika zidikha, fisi pambuyo ali: ‘igwa n’tola’.

“Mayi adakwera mapiri, kutsika mapiri, fisi pambuyo: ‘igwa n’tola’.”

Uwutu udali ulaliki wogwira mtima chifukwa fisiyo adatsatira mayiyo, koma nyama osagwa. Mapeto ake, fisi adafa ndi njala komanso kutopa.

Izitu ndidakumbukira chifukwa cha mapemphero adali pa Wenelapo. Kudali mwana wa munthu ndipo mumtima ndidati: Awa kutengeka ngati fisi. Igwa n’tola.

“Alleluya! Idzani kwa ine nonse osauka mudzachita bwino. Bwerani kwa ine akuchita kusaweruzika ndifufute machimo anu ndi labala uyu! Inde nonse ochita chigololo ndikukhululukirani. Muone lero mirakuli,” adatero wolalikayo.

Adali wamfupi, koma momwe adayambira kutalika! Adatalika, kutalika mpaka mutu wake udasowa m’mitambo. Tonse tidazizwa.

Posakhalitsa adabwerera mukufupika kwake.

“Ndaona ndithu zobwera mawa m’mitambomo. Ndaona kuti njala yonse itha ndipo Moya Pete palibe awachitirenso nsanje chifukwa chotenga abale awo onse kukaonera kukumana kwa Omaba ndi Papa ku Orleans. Inde, ndaona mankhwala azitsamba akupezeka ponseponse anthu kusiyanso kudalira zipatala zopanda aspirin.

“Inde, ndaona mitengo ya zinthu ikutsika mochititsa chidwi komanso ndaona Lazalo Chatsika akutsutsa molimbika zolakwa za Moya Pete. Komanso ndaona madzi, magetsi zikusefukira pano pa Wenela ngati madzi a mu Shire,” adapitiriza.

Akutero nkuti akuseweretsa foni yake yam’manja. Idalitu mose walero.

“Kuti tikhululupirire kuti si zadziko lapansi mukuchitazi, jambulani chithunzi pogwiritsa ntchito kafoni kanuko,” adatero Abiti Patuma.

“Indetu indetu ndinena ndi iwe Patuma Didimo. Ndimakudziwa! Nanga dzina lako ndalitenga kuti?” adafunsa mlaliki.

Ndidazizwa naye.

“Akulu, mwaiwala mudandionetsa chipsera chili pamsana panu tsiku lina m’nyumba yogona alendo ija? Jambulani chithunzi ndi foni yanuyo basi,” adayankha.

Mlaliki uja adaimika foni yake n’kuyamba kujambula mlengalenga ndi kafoni kake. Adationetsa chithunzi chomwe adajambulacho.

Padali nkhope ya mkulu uja wotchuka, Fula Kasamba.

“Aaaargh! Ukutionetsa Fula, kodi si mnzako ameneyo? Udajambula kalekale chithunzi chimenecho. Zanu n’zimodzi,” adatero Abiti Patuma.

“Komanso uyo Fula ukuti wajambulayo ali kozizira ati chifukwa adati woweruza ndi Alice in Wonderland. Izi akuti adazitenga pa Yobu 13:11,” ndidatero.

Koma akadadziwa! Mkulu uja adachita ngati akuuluka, n’kuyamba kuyenda m’malere.

“Indetu, ndinena ndi inu akusowa chikhulupiriro. Kodi iye wakuyenda pamadzi ndi iye wakuyenda mumlengalenga, wamphamvu ndani?” adafunsa.

Abale anzanga, apa mpomwe ndidadzidzimuka kumalotowo.

Gwira bango, upita ndi madzi!e!

Related Articles

Back to top button