Off the Shelf

Mlandu wa chisankho wafikapo

Umboni wa mboni yomaliza ya Pulezudenti wachipani cha Malawi Congress Party (MCP) Daud Suleiman wabweretsa mbudya za nyawani ku magulu onse okhudzidwa pamlandu omwe chipanicho chikuti sichinayende mwa chilungamo.

Iye adapereka umboni wake pogwiritsa ntchito makina a kompyuta, zomwe sizichitika kuno ku Malawi ndipo adaonetsa zomwe zidachitika pa kuwerengera mpaka kuulutsa zotsatira za Pulezidenti pa chisankho cha pa 21 May 2019.

Adapereka umboni wake: Suleiman

Kutsatira umboniwu, patuluka ndemanga zosiyanasiyana kuchokera kwa otsatira zipani za Democratic Progressive Party (DPP), Malawi Congress Party (MCP) komanso anthu apadera ongotsatira zomwe zikuchitika pa mlanduwu.

Ndemangazi zikusonyeza kuti otsatira MCP atafuna mbudya zotsekemera, otsatira DPP atafuna mbudya zowawasirako pomwe ambiri ongoyang’anira akuti nkhondo ikadalipo ngakhale chipani cha MCP chikuwoneka kuti mboni zake zathyakula bwino.

“Tayiphula, amati atani? Angatibere poyerayera amaona ngati ndife ana eti? Apapa kuvotanso kulipo basi afune asafune ndipo ulendo uno tiwaonetsa kadamsana,” watero wina otsatira chipani cha MCP Joseph Ganizani pa mchezo wa pa Intaneti.

“Suleiman wangopereka umboni koma si katakwe pa nkhani za makompyuta. Anzake enanso ozitsata apereka umboni wawo ndipo aonekera ndi wotsalira pankhanizi,” watero Emmanuel Kilowe wotsatira DPP pa Intaneti pomwepo.

Koma katswiri wina oona momwe zinthu zikuyendera Henry Kachanje wati padakalipano MCP ili ndi umboni wamphamvu omwe a DPP ndi Malawi Electoral Commission (MEC) akagona tulo sakwanitsa kuufafaniza.

“Umboni wa Suleiman waonetsa ndondomeko yonse momwe idayendera ndipo chabechabe, mpovuta kutsutsa umboni umene uja. Komabe mlandu amaweruza ndi majaji kotero ife tilekere pomwepa,” watero Kachaje.

Muumboni wake, Suleiman adaonetsa momwe anthu omwe sagwira ntchito kubungwe la MEC amalowera m’chipinda chomata cha MEC pa Intanet n’kumasintha komanso kufufuta zina ndi zina zomwe akukhulupilira kuti zidapotoza zotsatira za chisankho.

Chipelekereni umboni wake Suleiman, kubwalo lapadera ku Lilongwe kwakhala kukubwera nantindi wa anthu kukamvera ndi kuwona umboniwo.

Pano, zipani zosuma za MCP ndi UTM zamaliza kupereka umboni wawo ndipo osumilidwa DPP ndi MEC alowa m’bwalo kuyamba ndi mboni ziwiri za DPP zomwe ndi nduna ya maboma ang’onoang’ono ndi chitukuko cha m’midzi Ben Phiri yemwenso ndi mkulu woyendetsa za zisankho ku DPP komanso wazamalamulo Bob Chimkango.

Pamlanduwo, Saulos Chilima wa UTM ndi Lazarus Chakwera wa MCP adakasumira DPP ndi MEC kuti adasokoneza zotsatira za chisankho cha Pulezidenti zomwe akuti wapampando wa MEC Jane Ansah adapatsa mpando Mutharika.

Atsogoleri a zipani ziwirizi akufuna kuti chisankho chichitikenso ndipo pali mphekesera zoti mwina zipanizi zidzaphathana pachisankho chobwerezacho.

Malinga ndi majaji amene akumvera mlanduwo ati pofika pa 6 December akhala atapereka chigamnulochawo.

Related Articles

Back to top button