Chichewa

Mlandu wa Savala ukupendekeka

Listen to this article

 

Mlandu wa mayi wa zaka 33, Caroline Savala, yemwe khothi lidamupeza wolakwa pamlandu wakuba ndalama za boma zokwana K84 miliyoni ukuyenda mwapendapenda.

Savala yemwe amachita bizinesi ya zomangamanga adamupeza wolakwa ndipo akuyembekeza chigamulo cha khothi pa zachilango chake koma Lachisanu lapitali kudali ngati sewero ku bwalo la milandu pomwe womuimira pamlanduwo Ralph Kasambara adalephera kubwera kubwalolo.

Sadayankhe funso ngakhale limodzi: Savala (kumanzere)
Sadayankhe funso ngakhale limodzi: Savala (kumanzere)

Kusabwera kwa Kasambara mmawa wa Lachisanulo kudakwiyitsa wogamula mlanduwo Fiona Mwale yemwe adaimitsa mlanduwo kuti upitirire 2 koloko masana.

“Nkhaniyi ipitirira 2 koloko masana ano kuti woimirira mayi Savala abwere ndipo ngati sabwera tikamba nkhani popanda wowaimira,”adatero Mwale.

Malingana ndi ndondomeko za ku bwalo la milandu, tsiku likakhazikitsidwa ndipo woimirira munthu pamlanduwo walephera kubwera pachifukwa chilichonse, amayenera kudziwitsa bwalo la milandulo nthawi yabwino kapena kutumiza okamuyimirira.

Mmawa wa Lachisanu, kalaliki wa kukhotilo adali kalikiliki kuyesetsa kulumikizana ndi Kasambara koma sizimatheke zomwe zidachititsa Mwale kuti asinthe nthawi ya mlandu.

Nthawi ya mlandu itafika 2 koloko masana, Kasambara sadaoneke kubwalo la milandulo ndipo mmalo mwake adatumiza womuimirira Tisilira Kaphamtengo, yemwe adapempha wogamulayo kuti mlanduwo awusuntheso poti iye samautsatira bwinobwino.

“Ine ndiwongoimirira a Kasambala omwe sakumva bwino m’thupi koma poti nkhaniyi sindikuyitsata bwinobwino ndimati ndipemphe kuti isinthudwe ndipo idzakambidwe tsiku lina,” adapempha Kaphamtengo.

Mwale adakana kumva pempholi ponena kuti zomwe adauza khothi Kaphamtengo zokhudza kusamva bwino mthupi kwa Kasambala amayenera kuuza bwalolo nthawi yabwino ndipo adati mlanduwo upitirirebe.

Mwale atanena izi, Kaphamtengo adapemphanso kuti alole kuti Savala asayankhe funso lililonse limene afunsidwe poopa kupotoza nkhani ndipo pempholi lidaloledwa.

Savala adafunsidwa mafunso 10 koma sadayankhepo ngakhale limodzi mpaka mlanduwo udayimitsidwa.

Savala adapezeka wolakwa pa 18 July 2015 wogamula yemwe adalinso Mwale atapeza umboni wakuti mayiyu amalandira ndalama zosagwirira ntchito kuchoka ku unduna wa zokopa alendo.

Savala,yemwe samagwira ntchito m’boma nthawi yomwe amaganiziridwa kuti amalandira ndalamazo, adauza bwalo la milandu muumboni wake kuti iye adachita kukokeredwa mu kangaude wachinyengowu ndi mkulu wina yemwe amagwira ntchito ku unduna wazokopa alendo Leonard Kalonga komanso mnzake wa ku ubwana Florence Chatuwa omwenso amayimbidwa mlandu omwewo.

Related Articles

Back to top button
Translate »