Chichewa

Mlonda wosolola ‘solar’ akwidzingidwa

Listen to this article

 

Pamene kampani ya Inovantis m’boma la Machinga imanyadira kuti izigona tulo tabwino chifukwa yalemba ntchito Ibrahim Justin, wa zaka 23, ngati mlonda woteteza katundu wawo ku ndipsi, kampaniyi sinadziwe kuti yatuma galu kumalondera nyama ya mbuzi yowotcha kale.

Wojambula wathu akuganiza kuti zidali  chonchi mukhoti
Wojambula wathu akuganiza kuti zidali
chonchi mukhoti

Wapolisi wotengera milandu kukhothi pa Liwonde Police Post, Ezekiel Kalunga, adauza bwalo la milandu la Liwonde kuti pa April 19 chaka chino akuluakulu a kampani ya Inovantis adakagwada kupolisi kukadandaula kuti chipangizo chopanga mphamvu ya magetsi kuchokera kudzuwa (solar panel) chidasowa pakampanipo.

Kafukufuku woyang’ana chipangizochi ali mkati mkulu wa alonda pakampanipo adakumana ndi munthu wina atanyamula chipangizocho, chimene adachizindikira kuti ndi cha kampani yawo.

Alonda onse adatengeredwa kupolisi ndipo atapanikizidwa ndi mafunso kuti adazembetsa chipangizocho ndani, Justin adavomera kuti ndiyeyo adasolola.

Kalunga adapempha khothi kuti limuthyape Justin ndi chilango chachikulu popeza khalidwe lakelo ndi lothawitsa anthu, makamaka a maiko akunja monga Inovantis, kudzakhazikitsa bizinesi zawo m’dziko muno.

Popereka dandaulo, Justin adapempha bwalo kuti limupatse chilango chochepa popeza iye ndi nsanamira ya banja lake.

Woweruza milandu, Esther Phiri, adagwirizana ndi Kalunga ponena kuti khaliwe lakuba limabwezeretsa chitukuko mmbuyo n

Related Articles

Back to top button