Nkhani

Mmera watuluka koma samalani, atero katswiri

Listen to this article

Mmera watuluka ndipo momwe zikuonekera alimi ambiri akhoza kuchita mphumi chaka chino zinthu zikapanda kusintha, makamaka pakagwedwe ka mvula. Koma katswiri wa zamalimidwe wati mvula ili apo, mpofunikanso kutsatira njira zoyenera paulimi.

Mkulu woyang’anira za ulangizi ndi njira zamakono zamalimidwe, Dr Wilfred Lipita, wati mmene mvula yayambira ndi mwayi wa alimi kutsata njira zoti asadzakumane ndi zomwe zidaoneka chaka chatha.Chimanga_maize

Poyankhula ndi Uchikumbe, mkuluyu adati, mwa zina, ino ndiye nthawi yabwino yoti alimi akhoza kukolola ndi kusunga madzi ambiri kuti kutabwera ng’amba mwadzidzidzi asadzanong’oneze bondo mmera wawo omwe watuluka kale bwinowu ukufota.

“Tiyeni tichilimike panopa pomwe mvula ikugwamu. Tiyeni tikolole madzi ambiri kudzera m’njira zosiyanasiyana zomwe timadziwa zija n’kusunga madzi ambiri chifukwa njira yokolola madzi ndi imodzi mwa njira zodalirika tsopano,” adatero Lipita.

Iye adati alimi asalole udzu kapena zitsamba kutasa m’minda chifukwa zimaononga chakudya cha mbewu mmalo moti mbewu zidye chakudya chokwanira ndi kukula msanga mothamangitsana ndi mvula.

“Mvula ndi yosadalirika iyi masiku ano moti ikamagwa chonchi ndi nthawi yoti alimi tiigwiritse ntchito osalola kuti mwayi utiphonye. M’munda mukangooneka udzu kapena zitsamba, lowamoni msangamsanga n’kupalira kuti chakudya chomwe chili m’nthaka chikhale cha mbewu zanu zokha,” adatero Lipita.

Mkuluyu adatinso pomwe pali mwayi wa manyowa kapena feteleza, alimi asazengereze kuthira koma motsatira malangizo ochokera kwa alangizi komanso momwe unduna wa zamalimidwe umanenera.

Nthawi zambiri mvula ikachuluka, mizere ndi mbewu zimakokoloka kaamba kosowa chitetezo monga chimzere chotchinga mmbalimmbali mwa munda, milaga ndi kukwezera mizere msanga.

“Mukaona kuti madzi akuchuluka m’munda dziwani kuti nthawi iliyonse mizere ndi mbewu zanu zikhoza kukokoloka ndiye njira yabwino n’kuunda chimzere chachikulu mmphepete mwa mundawo, kuika milaga kapena kukwezera mizereyo msanga madzi asadachuluke mphamvu.

“Malangizo a mtundu uwu amaperekedwa mwaulere ndipo ngati anthu akuona kuti pali vuto lililonse m’munda mwawo, kudera kwawoko kuli alangizi a zamalimidwe omwe ndi okonzeka kuwathandiza nthawi iliyonse,” adatero Lipita.

Mu Uchikumbe wathu sabata yatha, katswiriyu adalangiza alimi kuti abzale mbewu zocha msanga komanso zopirira ku ng’amba ndipo sabata ino wawonjezerapo kuti mmapando momwe mbeu zidakanika kumera ndi mofunika kupakizamo msanga.

Iye adati kupakiza msanga kumathandiza kuti mbewu zisasiyane kwambiri m’munda kuti zizilandira dzuwa ndi kuwala kofanana kuopa kuti zina zingatchingike ndi zinzake kaamba kochedwa kumera.

“Ndikhulupirira pano alimi amadziwa kuti kupatula mchere wa m’nthaka ndi madzi, mbewu zimafunanso dzuwa ndi kuwala kuti zizibiriwira bwino. Mbewu zokulira pamthunzi zimakhala zonyozoloka ndi zachikasu ndiye pachifukwachi, sipafunika kuti mbewuzo zizisiyana makulidwe ake,” adatero katswiriyu.

M’madera ena pano alimi akutsatiradi malangizo oterewa moti ena akupalira m’minda yawo kuchotsa udzu ndi zitsamba zosafunikazo potengera phunziro pa zomwe adaona chaka chatha chifukwa chodeweza pochita zinthu. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »