Nkhani

‘Mmodzi adayenera kusiya ntchito’

Listen to this article

Ku maintaviyu ndi komwe anthu amapezerako mwayi wa ntchito, koma kwa mtolankhani wa kanema ya Zodiak, m’chigawo cha kumpoto Angela Saidi  adapezerako mwayi wa banja.

Zaka 11 zadutsa tsopano kuchokera pomwe Saidi adakumana ndi mwamuna wake Isaac Banda ku maintaviyu a uofesala a kadeti ku Salima.

Isaac ndi Angela tsiku la ukwati wawo
Isaac ndi Angela tsiku la ukwati wawo

Malinga ndi Saidi, awiriwa adali asilikali ku madera osiyana ndipo amakayesa mwayi wawo wokwera pantchito, pomwe Banda adachita naye chidwi.

“Apa tidayamba kucheza ngati chinzake ndithu. Padalibenso maganizo oti tsiku lina anthu nkudzavina,” adatero Saidi.

Iye adati mwa awiriwo,  Banda adakhonza maintaviyu ndipo adamutumiza ku Taiwan kukaphunzira za uofesala.

Saidi adati awiriwa amachezabe palamya komanso akabwera kumudzi patchuthi mpaka pomwe adamaliza maphunziro ake m’chaka cha 2010.

“Kwa zaka 5 tidali  pa chinzake ndithu, kufikira pomwe  adabwereratu ndipo ubwenzi wathu udayamba,” adalongosola motero Saidi.

Iye adati apa mmodzi mwa iwo amayenera kusiya ntchito malinga ndi malamulo a asilikali oti bwana ndi juniyo sayenera kupanga chibwenzi.

Malinga ndi Saidi, iye monga juniyo, adazitaya m’chaka cha 2012 atagwirako kwa zaka 10.

Awiriwa adakwatitsa pa 28 December m’chaka cha 2013 ku Kamuzu Barracks CCAP ndipo madyerero adachitikira ku Capital City Motel ku Lilongwe. Pano si Saidinso koma Angela Banda. n

Related Articles

Back to top button
Translate »