Chichewa

Mnyamata asiya sukulu chifukwa cha mantha

Listen to this article

 

A makhumbira atakhala msirikali, koma popanda moyo ntchitoyi singatheke. Lero Christopher Robert, mnyamata wachialubino, wasankha kaye moyo posiya sukulu yomwe ati ikadamuphetsa.

Zochitika pa 6 May 2016, pamene mnyamata wina wosamudziwa adafika pasukulu pawo kudzamutenga ndi zomwe zachititsa kuti thupi la Christopher lichite tsembwe ndi mantha kuti moyo wake ukhoza kukhala pachiswe ndipo walembera aphunzitsi ake kuti wasiya sukulu.

Mphunzitsi wamkulu pasukulu ya Mwatonga, kwa T/A Kasumbu m’boma la Dedza, wauza Msangulutso kuti patsikulo mnyamata wina adafika pasukulupo n’kunena kuti watumidwa kudzamutenga Christopher, wa zaka 18, yemwe ali kalasi 6, chifukwa akumufuna kupolisi ya Dedza.

“Amati watumidwa, koma nditaimba kupolisi, adandiuza kuti ndimumange, ndipo ndidaterodi,” adatero mphunzitsiyu, Felix Mussa.

Akuti moyo wake uli pachiopsezo: Christopher
Akuti moyo wake uli pachiopsezo: Christopher

Adatsagana ndi mayi ake a Christopher ndi achitetezo cha m’mudzi ulendo kupolisi komwe ati adakadzidzimuka akuuzidwa kuti amupepese mnyamatayo chifukwa chomunjata popanda chifukwa.

“Ine limodzi ndi mayi a Christopher komanso achitetezo tidamupepesa ndipo adamumasula pomwepo,” adatero Mussa.

Mnyamatayo, yemwe ndi wabisinesi, adauza Msangulutso kuti: “Adati ndikatenge amfumu, makolo a mwana ndi mwanayo kuti abwere kupolisi adzafunse zina ndi zina chifukwa amati kunyumba kwawo kudapitako anthu amene ankafuna akamube,” adatero iye.

Mathedwe a nkhaniyi adatutumutsa Christopher ndipo mantha adayanga thupi lake n’chifukwa adaganiza zolembera mphunzitsi wamkuluyu kuti sukulu waisiya.

“Zikomo Ahedi. Muli kudziwitsidwa kuti ndayamba ndasiya sukulu chifukwa cha nkhani yomwe inachitika Lachisanu. Ndiye ndaona kuti sindingathe kuphunzira chifukwa ndingathe kumakhala ndi maganizo komanso poweruka ndimakhala ndekha ndiye njira ndiyaitali chosadziwika chondichitikra munjiramu pamene ndili ndekha paja poyamba ndinafotokoza kale ndiye panopa ndili pankhawa ngati pangakhale kusamvetsa pazomwe ndanenazi munene tsiku kuti ndibwere kuti tidzakhambirane. Zimene ndinafuna kudziwitsani ndi zomwezi. Ndine Christopher,” ikutero kalaya yomwe adalemba Christopher.

Mtolankhani wa Msangulutso atamupeza kunyumbako, kudali kovuta kuti alankhulane naye.

Adadzitsekera m’nyumba, ngakhale ahedi a Mussa, amfumu komanso achibale ena adamuuza kuti asaope, iye adakanitsitsa poganiza kuti mtolankhaniyu wabwera kudzamuba.

Padatha mphindi 30, ndipo Christopher adatuluka, mayi ake atakambira naye. Nkhope yakugwa,    iye    adakhala patali ndi mtolankhaniyu.

“Ndili wachisoni kuti ndasiya sukulu. Ndimakhumbira nditakhala msirikali, koma basi sindidzakhalanso msirikali chifukwa sukulu ndasiya,” adayamba kufotokoza Christopher, amene adakhala nambala 4 m’kalasi teremu yatha.

Iye adati sakuganizanso atabwerera kusukulu chifukwa chilungamo sichidayende pankhani yake.

“Ndi bwino andiphere pakhomo pano kusiyana kuti akandiphere kusukulu. “Izi zidandipatsa mantha ndipo ndidaganiza zolemba kalatayo kuti ndasiya sukulu. Nakonso kukwaya sindikupita ndipo ndikungodzitsekera m’nyumbamu,” adatero Christopher, amene bambo ake banja lidatha ndi mayi ake.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Dedza, Cassim Manda, adavomera kuti mnyamata amene adapita kusukulu ya Christopher adamutulutsa chifukwa “adamangidwa mlandu wosaudziwa”.

“Tikufuna tifufuze kaye ndiye tamutulutsa. Kungoti pali zomwe zidachitika ndiye tikufufuza,” adatero Manda, ponena kuti sangayankhe mafunso ambiri pafoni koma pamaso.

Ngakhale mutu weniweni wa nkhaniyi sukudziwika bwinobwino, Christopher akuti sabwereranso kusukulu, komwe amayenda makilomita 7 kuchoka kunyumba kwawo.

Padakalipano mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wapempha amipingo kuti athandizepo kuti mchitidwe wopha ndi kusowetsa achialubino otheretu.

Anthu ena amakhulupirira kuti mafupa ndi ziwalo za anthuwa ndi zizimba za mankhwala olemeretsa. n

Related Articles

Back to top button
Translate »