Chichewa

‘Mnzanga ndiye adandipezera’

Listen to this article

 

Sylvester Namiwa, mneneri wa pulezidenti Peter Mutharika lero ndi wokondwa kwambiri kuti ukadaulo wa mtolankhani wa Nation, Albert Sharra, wamupatitsa mkazi amene adamanga naye ukwati pa 12 March 2016.

Namiwa akuti zonse zidayambika pamene iye adadwala, umotu ndi mu 2009 akukhala ku Malangalanga mumzinda wa Lilongwe.

Sylvester ndi Molly tsiku la ukwati wawo
Sylvester ndi Molly tsiku la ukwati wawo

Panthawiyo, Namiwa mnzake wapamtima, Sharra, akuti adapita kukamuona ndi kumuguliranso mankhwala.

Poona momwe Namiwa amavutikira chifukwa ankakhala yekha, Sharra adamulangiza kuti apeze wokhala naye, ngakhale panthawiyo Sharra sadamasule thumba la tambe.

Koma Namiwa akuti adamufunsa Sharra mozizwa ndi malangizo ake: “Ndani angandilole, ayise, taona momwe ndikuvutikira ndiye angandilole ndani?”

Macheza a awiriwa akuti adathera pa njole ina yotchedwa Molly Kenamu yomwe panthawiyo imakhala moyandikana nyumba ndi Namiwa koma kwawo ndi ku Bawi, kwa Senior Chief Makwangwala m’boma la Ntcheu.

“Ndidamuuza Sharra kuti namwaliyu sangalole kukhala pa ubwenzi ndi ine,” adatero Namiwa.

Koma Sharra, malinga ndi ukatswiri wake ngakhale nayenso sadakwatire, akuti adauzitsa Namiwa kuti zitheka. Njira adazipezadi Sharra ndipo ndi madzi amodzi, Molly adamwetulira. “Osadziwatu kuti Sharra panthawiyo adali atakambirana naye kale Molly,” adatero Namiwa.

Namiwa akuti sadavutikenso kusula mbalume chifukwa Sharra adali atakonza kale kapansi ndipo pakutha pa sabata ziwiri Molly adali atazizira nkhongono kuvomereza kuti asamala Namiwa mpaka m’manda.

“Chibwenzi chidayamba mu March 2010, mu July ndidamutenga kuti makolo anga akamuone. Chinkhoswe tidapanga pa 5 August 2010 ndipo nthawi yomweyo ndidamutegeratu. Pano tili ndi mwana wamkazi, Mwakamwereti, yemwe ali ndi zaka 5,” adatero Namiwa.

Koma Sharra akuti Namiwa amafuna akhazikike kotero amafunika mkazi woti akwaniritse loto lake.

“Ndinadziwa kuti Molly ndi mkazi yekhayo amene akadakwaniritsa khumbo lake ndipo ndine wokondwa kuti zili chonchi,” adatero iye.

Related Articles

Back to top button
Translate »