Nkhani

Moto wayaka ku Nkosini

Listen to this article

Pasanadutse n’komwe mwezi chilongere Inkosi Yamakosi Gomani Yachisanu ku Ntcheu, fumbi labuka pomwe mbali ina kubanjalo ikukakamiza wogwirizira, Rosemary Malinki kutula pansi udindo komanso kupepesa ati pa chipongwe chomwe adatulutsa pa mwambo wolonga ufumuwo.

Mbaliyi yati Malinki adalankhula ngati kulibe mawa ku mwambo wolonga Mswati Willard Gomani kukhala Inkosi Gomani yachisanu—kapena kuti Ngwenyama— pa 5 Ogasiti ku Nkosini, likulu la ufumu wachingoni—ku Lizulu m’bomalo.

Mneneri wa okhumudwawo, Dingiswayo Romeo Samson Philip Gomani, wauza Tamvani Lachiwiri m’sabatayi kuti tsopano abanja akukumana kukalondolera momwe ufumuwo uziyendera.

Koma Malinki wati angapepese pokhapokha nkhaniyo itafika ku Nkosini kwa Gomani.

Malinki wati ndi Ngwenyama yokha ili ndi mphamvu yochotsa kapena kusankha yemwe akuyenera kugwirizira ufumuwo.

Dingiswayo wati mwa zina, Malinki adaphotchola pomwe amaunikira kuti mkazi naye akhoza kulowa ufumu wa Gomani pofanizira Namlangeni, yemwe ati adalamulira ngakhale adali mayi.

Chatsitsa dzaye

Malinki adanyanyula mbaliyi ati popitiriza kuti Namlangeni “amalamulira amuna enieni osati amasiku anowa.”

Dingiswayo wati Malinki adapitirizanso kuti ufumuwo supita kwa ana omwe mayi awo sadalowoledwe, zomwe ati zidawanyanyulanso.

“Pachingoni, ufumu wathu umakhala m’nyumba imodzi; susinthana. Umakhala nyumba yomweyo mpaka Yesu adzabwere,” adatsendera Malinki.

Apa abanjawa, motsogozedwa ndi Dingiswayo, adatulutsa uthenga m’nyuzipepala Lachisanu pa 10 Ogasiti, kulengeza kuti Malinki apepese.

Dingiswayo, pouza Tamvani adati mkazi sangalamule pa ufumu wa Gomani komanso Malinki sakuyenera kukhala wogwirizira pomwe mfumu yadzozedwa.

Iye adatinso Malinki adalowoledwa kotero za ufumu wa Gomani sizikuyeneranso zimukhudze.

“Gomani IV adasiya ana atatu ndipo womaliza ndi Mswati koma onsewo akuchokera kwa amayi osiyana.

“Ubwino wake ana onse timakhala nawo pamodzi ngati mbumba.

“Mawu onena kuti ufumuwo supita kwa ana obadwira [kunja kwa banjalo] adatikwiitsa. Ichi n’chifukwa tikuti apepese,” adatero Dingiswayo.

Koma titamufunsa kuti achita chani ngati zokambiranazo sizichitika, iye adati ‘imeneyo ndi nkhondo’ komabe iwo ayesetsa kuti zokambiranazo zitheke.

Pa za mafumu achingoni achikazi monga T/A Kachindamoto, iye adati akudziwa za ufumu wa Gomani.

Koma mfumu yatsopanoyi idati singalankhule kanthu.

“Sindikudziwa yemwe angalankhule pankhaniyi. Padakakhala zoti dziko lidziwe tikadakuuzani,” idatero Ngwenyamayo.

Boma sililowerera

Nduna ya maboma aang’ono ndi chitukuko cha kumudzi, Grace Zinenani Maseko, yati boma sililowerera chilichonse pa nkhaniyo.

Maseko adati zomwe agwirizane a banja boma limvera zomwezo.

“Kaya asankha wina wogwirizira pomwe Mswati akupita kusukulu ife tivomereza,” adatero.

Mbiri ya ufumu wa Gomani

Philip Gomani yachiwiri idabereka Willard, Samson, Lineti, Hastings, Simasi, Titus ndi ena. Willard yemwe adali Gomani wachitatu adabereka Rosemary ndi Kanjedza yemwe adaali Gomani yachinayi. Kanjedza adabereka Frank, Zwelithini ndi Mswati yemwe ndi mfumu pano koma anawa adabadwa kwa amayi osiyana.

Samson adabereka Dingiswayo yemwe akukakamiza kuti Malinki apepese.

Related Articles

Back to top button