Chichewa

Mowe Pati: Amuna ndi dothi

Listen to this article

Tsikulo, mkulu wina adati tipite m’tauni tikaone umo zikukhalira chifukwa mikangano ya oitanira basi komanso oyang’anira mzinda ikukhala bwanji. Tidafika kumasitandi kumenetu kudali nkhondo yaikulu ati kulimbirana kuti amaminibasi ziwathera bwanji. Kodi azilipira kuti?

Vuto lidalipo ndi lakuti kodi oyendetsa minibasi ndi mabwana awo, angakhale ndi zikwanje zakuthwa ndani?

Zitayeni.

art

Lidali tsiku la amayi padziko lonse ndipo tidakhala malo aja timakonda pa Wenela. Adatulukira Mowe Pati kuchoka kwawo kwa Mkando, apooo!

“Kweeni, munasowatu zedi. Zikuyenda bwanji?” adafunsa Gervazzio, wapamalopo.

“Ndilipo. Kodi mwakumbuka zija ndinkanena za agalu athu ndi zothamangitsa anthu a ku China? Zija ndinkanena kuti atibwezere agalu athu. Ndidali mwana masiku amenewo,” adatero Mowe Pati.

“Koma mwati amuna ndi chiyani?” adafunsa Abiti Patuma, uku akumvera nyimbo ya Nilibe Pulobulemu.

“Abale, amuna ndithu ndi dothi. Ndipo musamawatchule kuti amuna ndi ana monga mwakhala mukunenera. Zitheretu,” adatero Mowe Pati.

Inu, ndithu kumanja kudali Coca-Cola, koma ankamwa Fanta munthu wa mayi.

“Aaaaargh! Mowe, mukunena zoona? Munganene kuti amuna ndi dothi? Chifukwa chiyani?” adafunsa Abiti Patuma.

“Eya, amuna ndi dothi, nanga si Mulungu adawalenga kuchoka kudothi!” adayankha.

Koma kuganiza kwinaku ungamangoti munthu uyu amasuta wamkulu fodya.

“Tsono mukatero, ndiye kuti bambo a kunyumba aja nawonso ndi dothi? Nanga ana anu aamuna aja nawonso ndi dothi?” ndidafunsa.

“Mwati bwanji?” adafunsa Mowe Pati.

“Ndikuti, mukamati amuna ndi dothi mukutanthauza kuti uja adaimba nyimbo ya Nilibe Pulobulemu mokopera, inde Moya Pete, nayenso ndi dothi?” adafunsa Abiti Patuma.

Mowe Pati adangoti duu! Ngati akumangidwa madiledi.

Abale anzanga, inetu izi sindingayankhireko kanthu. Kodi si ngati zija amanena za kunena kwa ndithendithe Nanthambwe n’kudzitengera.

Dr Getu Getu wa Moya Pete.

Gwira bango iwe, upita ndi madzi! n

Related Articles

Back to top button
Translate »