Chichewa

Moya Pete wagwa nayo

Listen to this article

 

Abale anzanga, lero palibe kucheza pa Wenela. Musandifunsenso kuti chifukwa chiyani chifukwa sindingakuuzeni.

Kodi simukudziwa kuti zinziri zinalowa pachipatala choyandikira pa Wenela? Abiti Patuma ndiye adandiuza kuti zibakera zinavuta mu Chilekamu mpaka ena kugonekedwa m’chipatala.

art-2

Kaya ndewuyo inali ya m’banja, kaya zachibwenzi koma kudali kusinjana ngati wina wagundidwa ndi sitima kuseri kwa Wenela.

“Koma amukwapula. Ena akuti mpaka mutu sukugwira ntchito mpaka kuthawa kuchipatala. Zovuta,” adatero Abiti Patuma tsikulo.

Koma n’sakutayitseni nthawi ndi zokamba za Abiti Patuma. Chifukwatu iyeyo ndi mnzake wa Mori wokunthidwayo. Komanso uyu Marison wokunthayo ndi mnzake ndithu. Iyetu adaphunzitsa ambiri kuti mowa sukuyenera kulepheretsa munthu sukulu komanso sukulu isalepheretse munthu mowa.

Tsonotu lero sikuti pali zonena za pano pa Wenela chifukwa ndatopa nazo. Ndalema. Ndikudabwa. Kodi mukuti kuli Moya Pete? Abale anzanga, nkadakhala mkuluyu nkadasiya zonse.

Sizikuyenda. Magetsi kulibe. Madzi nawo ndi anjomba. Kunena za kuchipatala, mankhwalanso kulibe.

Lero akuti tizidya kamodzi tikakhala ku Wodi 3B. Eti ngati tili kundende.

Mkulu zamulaka. Walephera. Sanakhoze.

Titambasule za madzi. Nanga lero munthu nkumanena kuti ndi bwino kumwa madzi pachitsime? Lero lino kutunga madzi padilawo nkukhala munthu wolemekezeka?

Walephera. Apondeponde akaone zina ku America kuli ana akeko.

Nanga lero munthu nkumakamba za koloboyi, ati madzi achepa mu Shire? Dzulo ndi dzana adatiuza kuti madzi achuluka zedi moti sangathe kutapa magetsi. Lero akutinji?

Walephera.

Nanga taonani umu akudulira mitengo! Ngakhale muwauze alonda a nkhalango akhale ndi mfuti, ateteza chiyani? Mitengo idatha.

Walephera.

Kunena za malata, simenti ndi zina zija adalonjeza kuti adzatsitsa, zakwera mtengo chifukwa ndalama yake akulephera kuigwira.

Walephera.

Nanga tinene za mpira wa zikhatho, inde mpira wa mafumukazi! Nanga kulephera tinene kuti nkukhoza? Kuchinyidwa tinene kuti nkuwina?

Walephera mwana akagone.

Sindinganenenso za uchifwamba chifukwa uko ndiye wagwa nayo zedi. Walephereratu.

Zilo pa 10.

Walephera mwana akagone.

Kumaphunziro sinditaya nako nthawi. Kungotsegulira Poly, anyamata ali pamsewu.

Walepheranso.

Nanga chilungamo? Alibe chilungamo. Wakuba ana, ati akakhale kumalo aja ozizira zakaziwiri. Mbali inayi, wokwapula mkazi wake, ati akakhale pashamba zaka 13 ndi theka.

Walephera ndithu.

Zisiye iwe.

Mpake kusadabuza anzake. Ati uyu Koko nkukamusiya athane ndi mafumu aja a m’tauni akuvutawa! Uyu Atipatsa Likhweru ndiye kumusuntha moti ambiri pano pa Wenela akuti Moya Pete akumuyesa ndi kumuphunzitsa zonse chifukwa iye wakalamba. Wachembera! Nanga uyu wamankhwala, mayi wathu wa ku Mponela, make Chinyau, kumuletsa kusolola mankhwala lero ali pati?

Gwira bango, upita ndi madzi!!n

Related Articles

Back to top button
Translate »