Nkhani

Moyo pachiswe: Ambiri akuzemba mankhwala otalikitsa moyo

Listen to this article

Amati phukusi la moyo umadzisungira wekha, koma kumene zikuloweraku, zikuonetsa kuti Amalawi ambiri omwe ali pamndandanda wolandira mankhwala otalikitsa moyo (ma ARV) akukwirira phukusi lawo pachulu cha agang’a pozemba kulandira ndi kumwa mankhwalawa.

Malingana ndi zomwe Tamvani yapeza kuchokera kumgwirizano wa mabungwe olimbana ndi kufala kwa kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi, anthu 20 mwa anthu 100 alionse oyenera kulandira mankhwalawa akuchita ukamberembere.

Mankhwala otalikitsa moyo ngati awa safuna kudukiza munthu akayamba kumwa
Mankhwala otalikitsa moyo ngati awa safuna kudukiza munthu akayamba kumwa

Wapampando wa mgwirizanowu, Maziko Matemba, wati ukamberemberewu ndi chiphe kaamba koti anthu otere sachedwa kugwidwa ndi chipwirikiti cha matenda chifukwa chitetezo cha m’thupi mwawo chimatsika msanga.

Matemba adati kupatula kutsika kwa chitetezo cha m’thupi, anthu omwe amati kuyamba kumwa mankhwalawa n’kudukiza thupi lawo limapima kotero kuti silimvanso mankhwala alionse omwe angalandire akamva.

“Tili ndi nkhawa yaikulu kwambiri chifukwa anthu otere ndiwo amabwezeretsa chitukuko cha dziko mmbuyo. Boma likuyesetsa kugula mankhwala kuti anthu ake azikhala nthawi yaitali ali ndi thanzi, koma iwo n’kumathawanso, komwe kuli kusayamika,” adatero Matemba.

Iye adati abambo ambiri komanso omwe amakhala m’matauni ndiwo akuchulukira kuzemba mankhwalawa kaamba ka manyazi, kuiwala kuti ali ndi udindo pamabanja awo ndi dziko lomwe.

Mafigala a bungwe la Malawi Network of Aids Organisations (Manaso) amasonyeza kuti m’dziko muno muli anthu pafupifupi 850 000 omwe akuyenera kumalandira mankhwala otalikitsa moyo koma mwa anthuwa, m’madera akumidzi ndimo anthu ambiri amatsatira ndondomeko.

Mkulu wa Manaso, Abigail Dzimadzi, adati gulu lina lomwe likuchulutsa ukamberembere ndi achinyamata omwe safuna kuonekera kuti ali ndi kachilombo poopa kuti angadzasowe mabanja mtsogolo.

“Chiopsezo chachikulu chili poti munthu yemwe sakulandira mankhwala ndiye ali n’kuthekera kwakukulu kofalitsa kachilombo ndiye ngati achinyamata akuzemba, zikutanthauza kuti tikulimbana ndi nkhondo yomwe tikumenyananso tokhatokha,” adatero Dzimadzi.

Nduna ya zaumoyo, Dr Peter Kumpalume, akuti nkhaniyi ndi yomvetsa chisoni kaamba kakuti boma limafunitsitsa vutoli litatheratu m’dziko muno poti ena mwa anthu omwe dziko limataya chifukwa cha vutoli ndi ofunika mipando yautsogoleri.

Anthu ena auza Tamvani kuti nthawi zina anthu amazemba kukalandira mankhwala kaamba ka momwe amalandiridwira kuchipatala, koma unduna wa zaumoyo ndi bungwe la Manaso ati chifukwa ichi n’chozizira polingalira za moyo wa munthu.

“Mpofunika kuunika nkhani ya chinsinsi cha odwala chifukwa ena safuna kuonekera koma ali ndi mtima wofuna kumalandira thandizo. China ndi malankhulidwe a ogwira ntchito kuchipatala omwe amagwetsa anthu ulesi,” adatero Lucy Banda, wapampando wa gulu lophunzitsa ndi kuyendera anthu omwe ali ndi kachilombo ka HIV ku Senga Bay, komwe akuti abambo ambiri amazemba kulandira mankhwalawa n’kumatangwanika ndi usodzi.

Woyang’anira nkhani za umoyo muunduna wa zaumoyo, Dr Charles Mwansambo, wati ichi n’chimodzi mwa zifukwa zomwe boma, kudzera muundunawu, lidakhazikitsa pologalamu yoti kuchipatala kuzikhala malo apadera oti anthu azikalandirirako uphungu pankhani za Edzi ndi mankhwala otalikitsa moyo.

“Panopa m’zipatala zambiri muli malo apadera omwe anthu amakalandirirako uphungu, kuyezetsa magazi ndi kulandira mankhwala otalikitsa moyo. Ndiye nkhani ya chisinsiyo idakonzedwa,” adatero Mwansambo.

Iye adatinso boma lidakhazikitsa pologalamu ya ma 90 atatu (90 90 90) kufuna kuti anthu athe kuzindikira kufunika kwa kutsatira ndondomeko ya mankhwala a ARV.

Ndondomekoyi imatanthauza kuti anthu 90 alionse pa anthu 100 akudziwa momwe alili m’thupi mwawo; mwa anthu 90, 90 a iwo akulandira mankhwala otalikitsa moyo moyenerera; ndipo anthu ena 90 atetezedwa kukutenga kachilomboka.

Potsindika kufunika kolimbana ndi matendawa, naye sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Richard Msowoya, adapempha aphungu a nyumbayi kuti kupatula kudalira bajeti ya boma, azikhala ndi mapologalamu opezera zipangizo zomenyera nkhondoyi.

Pempholi adaliperekanso kwa akuluakulu a mabungwe pamisonkhano yomwe nyumbayi idachititsa mwezi wa August wa aphungu ndi amabungwe pankhani yolimbana ndi matendawa m’chigawo cha maiko a kummwera kwa Africa, yomwe imadziwika kuti Sadc-PF.

Related Articles

Back to top button
Translate »