Chichewa

MOYO UKUTHINA

 

Amalawi ena ati mavuto ankitsa ndipo akusowa mtengo wogwira pamene akadaulo a zachuma akuti mavutowa afikanso pena chifukwa cha njala imene ili m’dziko muno.

William Joseph wa kwa Manaseh mumzinda wa Blantyre, yemwe ndi mmodzi mwa Amalawi 62 mwa 100 alionse amene amapeza ndalama zosaposa K710 patsiku, kapena K21 000 pamwezi adati madzi afika m’khosi.

Ngakhale boma lidakhazikitsa kuti ogwira ntchito asamalandire ndalama zochepera K20 000 pamwezi, Joseph yemwe amagwira ntchito yaulonda, amalandira K15 000 pamwezi.

Bambo wa mwana mmodziyo adati: “Mavuto alipo. Tikukhala nyumba ya K6 500 pamwezi, kusonyeza kuti K8 500 yotsalirayo ndiyo timagwiritsa ntchito pogula ufa wa m’mawokumani, ndiwo ndi sopo. Ndiye tikumva kuti pakufunika ndalama zoposa K100 000 pamwezi kuti moyo uziyenda bwino…. Ha!”

Malinga ndi iye, kudya ndi kawiri patsiku basi pofuna kukokera.

Umphawi wafika pena
Umphawi wafika pena

Pambali pa mkazi wake, yemwe sagwira ntchito, banja lake limasunganso mwana wina, kusonyeza kuti nyumbayo muli anthu anayi. Iye adati vuto ndi lakuti onsewo maso amakhala pa iye, kaamba koti sakwanitsa kupeza mpamba kuti mkazi wakeyo ayambe bizinesi.

“Mwayi wake mwana wanga ali kusukulu ya pulaimale yomwe ndi yaulere. Khumbo langa nkuti nditapeza ndalama pafupifupi K50 000 ndipite kumudzi kukakhala apo ayi mwina ndiyambe bizinesi ngatitu ingakhale yaphindu,” adatero Joseph.

Naye Bridget Yonasi, wa kwa Che Mussa mumzinda omwewu, zinthu zaima makamaka chifukwa thobwa limene amagulitsa silikuyenda malonda kaamba ka chisanu chimene chabukachi. Iye wati akuvutika kupeza chakudya, ngakhalenso kulipirira sukulu mwana wake amene ali Fomu 3 kusukulu ya sekondale ya Namiwawa. Fizi kusukuluyo ndi K5 500.

Yonasi adati ngakhale wayamba ntchito yogulitsa m’golosale komwe akulandira K10 000 pamwezi, moyo ukadali kuthina. “Timagona ndi njala nthawi zambiri chifukwa chosowa ndalama zogulira chakudya. Ndimakhala nyumba ya K5 000 koma ndatulukamo chifukwa imadula ndipo ndalowa ya K3 000. Konsekotu nkuyesayesa kuti tidye komanso kupeza zofuna za anawa,” adatero iye.

Nkhawazi zikudza pomwe bungwe la Centre for Social Concern (CfSC), limene mwezi ndi mwezi limatulutsa ndalama zimene zimafunika kuti munthu akhale pabwino, lati ngakhale ndalamazo zidatsikirako mwezi wa June, anthu olandira ndalama zochepa kwambiri ngati Joseph ndi Yonasi adakali pamoto.

Malingana ndi chikalata cha CfSC, ndalama zofunika pamwezi pogulira zakudya ndi zina zofunika pamoyo zidatsika kuchoka pa K166 597 mwezi wa May kufika pa K165 660 mwezi wa June.

CfSC idati nkofunika kuti boma lilimbikitse ulangizi kwa alimi kuti dziko lizikhala ndi chakudya chokwanira chifukwa njala ndi umphawi zimayendera limodzi. Bungwelo lidalimbikitsanso boma kuti lizilimbikitsa Amalawi kukhala ndi njira zopezera ndalama, mmalo mowazoloweza kuwapatsa zinthu zaulere.

Katswiri wa zachuma kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Ben Kaluwa adati kutsika kwa ndalama zomwe anthu angagwiritse ntchito pamwezi mwezi wa June si zodabwitsa chifukwa nthawiyi Amalawi amakhala atakolola.

“Apa timayembekezera kuti ndalamayi imatsika kumene, koma taonani momwe yatsikira, palibe chiyembekezo apa kuti zinthu zikhala bwino. Ikadakhala kuti ndalamayi yacheperatu mwina tikadasangalala, koma apa yangotsika ndi ndalama yosaposa K1 000. Palibe chimwemwe,” adatero Kaluwa.

Iye wati pano tili mu July kusonyeza kuti zinthu zayambanso kukwera mtengo chomwe ndi chiopsezo kwa Amalawi chifukwa zinthu zifika poliritsa miyezi ikubwerayi.

Kaluwa adati Amalawi ambiri sapeza ndalama yoposa K50 000 pamwezi ngakhale zoloserazo zikukamba ndalama yoposa K100 000.

“Izi zikutanthauza kuli mavuto, ndipo tikuloweratu anthu alira koopsa chifukwa zinthu zikukwera mtengo tsiku lililonse komanso mtengo wa thumba la chimanga wakwera kwambiri,” adaonjezera motero.

Mkulu wa bungwe loona za momwe chuma chikuyendera la Malawi Economic Justice Network (Mejn) Dalitso kubalasa adati mavuto onsewa akudzanso chifukwa dziko lino silikupanga katundu ochuluka.

“Katundu wopangidwa m’dziko amayenera kukhala ochuluka kuposa amene akumufuna kuti mtengo ukhale wabwino. Bungwe la United Nations (UN) linkawerengera kuti anthu amene amagwiritsa ntchito ndalama yosposa K710 patsiku ndiye kuti ali paumphawi ndipo onani lero ndi Amalawi angati akugwiritsa ntchito ndalama yotere? Mupeza kuti ndi ochepa,” adatero Kubalasa.

Iye adagwirizana ndi Kaluwa kuti kutsogoloku kuli moto kuposa mmene zilili pano. “Vuto mvula yavuta ndipo takolola zochepa, zomwe zipangitse zinthu zikwere mitengo. Palibe kothawira,” adatero Kubalasa. n

Related Articles

Back to top button