Chichewa

‘Mpendadzuwa sulira madzi ambiri’

Mpendadzuwa ndi imodzi mwa mbewu zimene alimi angapindule nazo. HOLYCE KHOLOWA adacheza ndi Maxwell Chimombo wa m’mudzi mwa Cedrick kwa Ngwelero ku Zomba amene akulima mbewuyi. Adacheza motere:

Kodi mbewu ya mpendadzuwa imalimidwa bwanji?

Choyamba mlimi amaunga mizere yokula ndi kutalikana ngati ya chimanga. Kachiwiri, mlimi amayenera kukhala ndi mbewu yabwino osati yobwafuka kapena ya matenda kuopera kuti ingavute kumera. Akatero, mlimi azingodikira mvula.

Chimombo kusankha mpendadzuwa kuti akabzale

Kodi mpendadzuwa umabzalidwa ndi mvula yake iti?

Mpendadzuwa timabzala kawiri wina timabzala limodzi ndi chimanga mvula yoyamba ija ikangogwa pamene wina timabzala pakadutsa mwezi ndi theka chibzalireni mbewu zina zija chifukwa sumafuna madzi ambiri.

N’chifukwa chiyani mpendadzuwa sumafuna madzi ambiri?

Mpendadzuwa umene wabzalidwa ndi mvula uja ukamakololedwa wambiri umakhala mphwepwa chifukwa umakhala kuti udamwa madzi ambiri ali m’munda pamene wabzalidwa kachiwiri uja umakhwima mvula ikadukiza zimene zimachititsa kuti nthangala zake zikhale zangwiro zimene sizivuta malonda pa msika.

Mwachitsanzo, mlimi amene wabzala mpendadzuwa ndi mvula yoyamba akhoza kukolola matumba 20 koma akamazapeta akhoza kutsala ndi matumba 14 chifukwa chimachulukitsa matumbawo ndi mphwepwa pamene mlimi amene wabzala kachiwiri akhoza kukololanso matumba 20 koma akapeta mpendadzuwao akhoza kutsala ndi matumba 19 choncho mpendadzuwa wabwinoyu ndi wachiwiri.

Mwachitsanzo, chimanga changa ndinabzala mu November 2016 koma pano ndili pakalikiliki kulima komanso kusankha mbewu chifukwa mpendadzuwa ndibzala kumapeto kwa January uno kapena kumayambiriro kwa February.

Kodi mpendadzuwa mumabzala bwanji?

Timabzala motalikana masentimita 75 phando lililonse komanso pa phando pamayenera kubzalidwa nthangala zosaposera ziwiri kuti mpendadzuwa ukule motakasuka bwino komanso kuti usamaphangirane chakudya cha munthaka.

Mbewuyi ikamera imayenera kumasamalidwa bwino makamaka poyipalira mwakathithi kuti m’mundamo musakhale tchire limene ndi chiopsezo cha mbewu.

Dothi limene limakhala bwino kulimapo mpendadzuwa ndi lotani?

Mpendadzuwa umachita bwino m’dothi lililonse koma dothi la makande ndiye pachimake chifukwa limasunga madzi pamene dothi la mchengachenga mbewuyi imabereka mosisitika chifukwa madzi amalowa pansi msanga m’nthaka kusiya mbewuyi pamoto.

Kodi mpendadzuwa umagwidanso ndi tizilombo kapena matenda?

Mmmmmm pamenepo sindikudziwa bwinobwino chifukwa chiyambireni mpendadzuwa wanga sunagwidwepo ndi matenda. Chinsinsi changa ndi chakuti m’munda mwanga mumakhala mwaukhondo nthawi zonse zimene ndikukhulupirira zimathandiza kupewa matenda ndi tizilombo.

Ndi mavuto anji amene mumakumana nawo pa ulimiwu?

Vuto lalikulu ndi misika yodalirika ya mpendadzuwa chifukwa kwathu kuno amatigula mpendadzuwa ndi mavenda. Kuipa kwa mavendawa ndi kwakuti iwowo ndi amene amatipangira mitengo. Nthawi zambiri mavendawa akafika amatiuza kuti malonda a mpendadzuwa sakuyenda bwino kumisika ikuluikulu m’tauni choncho atigula pa mitengo yotsika. Ndiye chifukwa ife kumisika ikuluikuluko sitimakudziwa timangogulitsa pa mitengo imene mavendawo afuna.

Mwachitsanzo, mu 2016 alimi timafuna tikumagulitsa pa mtengo wosachepera K200 pa kilogalamu koma mavenda atafika kuno amatigula pa K170 zimene zinatiwawa kwambiri.

Vuto la kusowa kwa misikali mukuganiza lingathe bwanji?

Tikupempha eni makampani komanso akuluakulu a zaulimi m’dziko muno kuti abwere kwathu kuno adzadzionere okha mmene anthu tikulimira mpendadzuwa chifukwa kwathu kuno tiliko alimi ambiri komanso adzatipatse upangiri wa mmene tingamapezere misika yodalirika ya mpendadzuwa chifukwa mavendawa akutidyera masuku pamutu.

Tsimikizani kuti mpendadzuwa ndiwabwino?

Mpendadzuwa ndi wabwino chifukwa sumalira feteleza ngati mbewu zinazi komanso sumavuta malonda chifukwa anthu amene tikulima mbewuyi ndi ochepa. Ife malonda athu sabwerera kumsika chifukwa ofuna mpendadzuwa ndi ambiri pamene alimi a mpendadzuwa ndife ochepa. n

Related Articles

Back to top button