Chichewa

Mpendadzuwa ungatukule malawi

 

Mkulu wa bungwe la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda, wati pakuyenera kukhala ndondomeko yabwino pakati pa alimi, misika, komanso boma kuti mpendadzuwa uzilimidwa ochuluka.

Polankhula ndi Uchikumbe, iye adati makampani komanso makopaletivi omwe amagwiritsa ntchito mpendadzuwa popanga mafuta ophikira  atagwirizana ndi alimi komanso boma, mpendadzuwa ukhonza kumalimidwa mochuluka zomwe zingapangitse kuti mafutanso azipangidwa ochuluka.

Phindu la mpendadzuwa ndi losayamba

“Mafutawa akhonza kumagulitsidwa m’Malawi momwemuno ngakhalenso kunja,” adatero mkuluyo.

Izi zikugwirizana ndi zomwe adanena Cliff Chiunda, mlembi wamkulu muunduna wa za migodi, malonda ndi zokopa alendo mmbuyomu kuti dziko la Malawi lingapulumutse K3 biliyoni zomwe limaononga pogula mafuta ophikira kunja chaka chilichonse.

Kapichira Banda adati: “Ambiri akuthamangira kulima fodya chifukwa msika wake siuvuta. Pomwe fodya akulimidwa wochuluka, mitengo imatsika ndipo wina amabwerera. Ena akadamalima mpendadzuwa bwenzi akusimba lokoma,” adatero iye.

Iye adati boma limayenera kulimbikitsa alimi pa za mbewuyi ndipo mpendadzuwa ukupambana fodya chifukwa amapangira mafuta ophikira omwe pafupifupi aliyense amagwiritsa ntchito pomwe si onse amasuta fodya. Mkuluyo adaonjezanso kuti mpendadzuwa sulila feteleza ngati mbewu zina komanso m’munda mwa mbewuyi simumera udzu kwambiri.

Mathias Banda, wapampando wa kopaletivi ya Talimbika Agro-Processing and Marketing yopanga mafuta ophikira otchedwa Sunpower  kuchokera ku mpendadzuwa m’boma la Salima, adati anthu sakukhala ndi chidwi ndi ulimiwu.

“Tili ndi alimi athu omwe timawalangiza momwe angalimire mpendadzuwa ndipo pamapeto pake amatigulitsa  koma sukwanira kupangira mafuta chaka chonse kotero timayendayenda kusakasaka komwe tingaupeze. Tangoganizani, timachoka ku Salima kukagula ku Phalombe ndipo kumeneko ukatha timalowa m’dziko la Mozambique konseku kuli kusaka mpendadzuwa,” adatero Banda.

Iye adaonjeza kuti izi zimapangitsa kuti azipanga mafuta ochuluka m’nthawi yokolola yokha ndipo ikangodutsa amapanga mafuta ochepa. Iye adafotokozanso kuti mafuta awo ndi ovomerezeka ndi a Malawi Bureau of Standards (MBS) ndipo yapeza kale misika m’maiko a kunja koma nkhawa yawo ndiyoti azikapeza kuti mpendazuwa ochuluka.

“Mpendadzuwa suvuta kulima ndipo umacha pakutha masiku 60. Mlimi amangodikira masiku 10 owonjezera kuti ayambe kukolola. Pa ekala imodzi yokha mlimi akhonza kukolola makilogalamu 2000 akausamalira bwino,” adatero Banda.

Iye adaonjezanso kuti alimiwa akuyenera kulima mpendadzuwa pomwe mvula ikugwa yochuluka kuti awuteteze  ku anunkhadala.

“Anunkhadala amaononga mpendadzuwa ukangomera kumene makamaka ngati mvula siikugwa yokwanira kotero mlimi akhonza kubzala kangapo. Akabzalidwa pamene mvulayi ikugwa yochuluka, anunkhadala amasokonezeka,” adatero iye.

Banda adati mbewuyi imachita bwino paliponse koma imachita bwino kwambiri m’madambo. Iye adati mizere yake imayenera kutalikirana ndi masentimita 75 ndipo pobzala, utalikirane ndi masentimita 25 ngati ukubzalidwa umodziumodzi ndipo utalikirane, masentimita 45 kulekezera 60 ngati ukubzalidwa uwiriuwiri.

Iye adachenjezanso kuti mbewuyi imayenera kusamalidwa bwino kwambiri pokolola chifukwa siyichedwa kuola. Iye adati mbewuyi imadana ndi chinyezi komanso kuikidwa pamalo akuti pali tizilombo tomwe timayambitsa kuola. Mpendadzuwa ukaola, umatulutsa mafuta owawa choncho phindu limachepa. n

 

Related Articles

Back to top button