Chichewa

Mphini yobwereza Idawala mu 2020

Listen to this article

Chaka cha 2020 chidali chaka cha pelete chomwe podzuka m’mawa wa tsiku la pa June 27 2020, Amalawi adadzidzimuka kuona kuti omwe adali kutsogolo tsopano ali kumbuyo ndipo omwe adali kumbuyo ali kutsogolo ngati muja zimakhalira pa pelete wotsogolera akati tembenukani.

Izi zidatsatira chisankho chobwereza chomwe chidachitika pa June 23 2020 potsatira chigamulo cha khothi lomwe lidapeza kuti chisankho cha m’chaka cha 2019 sichidayende bwino ndipo chimayenera kubwerezedwa.

Kadaulo pa ndale Mustafa Hussein wati zomwe zidachitikazo zidasonyeza kukhwima kwa demokalase m’dziko muno chifukwa malamulo adagwiritsidwa ntchito posankha mtsogoleri.

Voti imapereka mphamvu kwa nzika zosankha atsogoleri a ku mtima kwawo

“Choyamba chisankho chidabwerezedwa chifukwa padapezeka kuti zofuna za anthu zidasemphana ndi zotsatira zachisankho cha 2019. Ichi n’chifukwa chake khothi lidagamula kuti Amalawi aperekenso maganizo awo kudzera m’kuvotanso.

“Chachiwiri zidapereka phunziro lalikulu ku bungwe loyendetsa zisankho komanso nthambi zina zokhudzidwa kuti lamulo ndiloyenera kutsatidwa paliponse. Akati chisankho ndi mwayi wa anthu eni ake kusankha osati wina kuwasankhira ayi,” watero Hussein.

Koma iye wati mpofunika kuunikira bwinobwino kuti ichi chisasanduke chizolowezi choti chisankho chilichonse chizikathera ku khothi chifukwa kutero n’kuvula mphamvu za anthu n’kuzipereka kwa makhothi.

“Zidakhala bwino kuchitika choncho koma likhoza kukhala vuto lalikulu ngati anthu angatenge kuti chikhale chizolowezi chifukwa pameneponso ndiye kuti demokalase yalephera,” watero Hussein.

Chisankho cha 2019 ndi zotsatira zake

Pa 21 May 2019 Amalawi adalawirira kukasankha makhansala, aphungu ndi mtsogoleri wa dziko lino, koma nyanga zidakola pa zotsatira za pulezidenti.

Pa May 27, 2019, bungwe la MEC lidalengeza kuti Peter Mutharika wa DPP adapambana pa chisankho cha pulezidenti cha pa May 21 2019.

Zotsatirazo zidapangitsa kuti Chilima ndi Chakwera akasume ku khothi kuti Mutharika ndi bungwe la MEC adasokoneza chisankho ndipo mpofunika kuti zotsatirazo zitayidwe m’madzi chifukwa sizimaimirira ganizo la Amalawi.

Chigamulo cha khothi

Chakwera ndi Chilima atakasuma ku khothi. Pa February 3 2020, khoti la Konsititushoni lidagamula kuti chisankho cha 2019 sichidayende bwino ndipo n’chofunika chitachitikanso.

Pogamulapo khotilo komanso la Apilo adatanthauzira kuti opambana pachisankho akuyenera kukhala ndi mavoti oposa theka la anthu onse omwe aponya votiyo (50%+1).

Makhotiwo adaunikiranso kuti Nyumba ya Malamulo ikakonzenso ndondomeko zoyendetsera zisankho kuti tanthauzo lakupambanalo likamveke bwino kupangira zisankho zobwera mtsogolo.

Zotsatila ku Nyumba ya Malamulo

Nkhaniyo itapita ku Nyumba ya Malamulo ndipo aphungu ataizukuta, adavomereza kuti opambana pa mpando wa pulezidenti azikhala ndi mavoti oposa theka la mavoti onse omwe aponyadwa ndipo ndondomekoyo imatchedwa 50% + 1.

Ndemanga za akadaulo pa malamulo ndi ndale

Koma pomasulira zomwe makhoti adanena ndi zomwe zidachitika ku Nyumba ya Malamuloyo, kadaulo pa za ndale Henry Chingaipe adati palibe chomwe aphunguwo adalakwitsa.

“Pamlandu wachisankho, khoti lidatanthauzira gawo 80 (2) la malamulo lomwe limakamba za chisankho cha Pulezidenti chokha basi osati aphungu kapena makhansala ndiye tanthauzo la 50%+1 lomwe khothi lidapereka lidangokhudza chisankho cha Pulezidenti,” adatero Chingaipe.

Pa za bilu yomwe nyumbayo idadutsitsa, Chingaipe adati cholinga chake chidali kukonza gawo 96 (5) la malamulo lomwe limakamba zachisankho cha Pulezidenti komanso aphungu kuti pa zisankho ziwirizi pakhale chiunikiro chomveka bwino.

 “Momwe biluyo idadutsa tsopano, gawo 96 lizineneratu kuti opambana chisankho cha Pulezidenti azipeza 50%+1 pomwe opambana pa uphungu azipeza mavoti oposa anzake pa chisankhopo. Apa ndiye kuti zisankho zonse zamtsogolo zaunikiridwa,” adatero Chingaipe.

Iye adagwirizana ndi kadaulo pa ndale George Phiri yemwe adati aphunguwo adachita zakupsa chifukwa khoti litagwira ntchito yake lidaona kuti mphamvu zake zafika pamalire ndipo kotsalako kumafuna nyumbayo kuti isinthe malamulo monga mwa mphamvu zake.

Mwa zina biluyo ikunena zoti pazipita masiku apakati pa 7 ndi 30 Pulezidenti asadalumbire akasankhidwa komanso kuti aphungu omwe alipo panowa akhala zaka zisanu n’chimodzi (6) m’malo mwa zisanu (5) kuti chisankho china cha aphungu chidzachitike limodzi ndi cha Pulezidenti m’chaka cha 2025.

Related Articles

Back to top button