Chichewa

Msewu wa Rumphi-Nyika udzatheka?

Mkonzi,

Ndafuna ndipereke chidandaulo kuboma lathu kudzera m’nyuzi yathuyi komanso kwa phungu wa dera lathu la Rumphi West Hon Jacquilline Kouwenhoven kuti atiganizire za msewu wa Nyika womwe wakhala zaka zambiri osauganizira chonsecho ndi msewu wofunika kwambiri pachitukuko cha dziko lino, maka kumbali yokopa alendo.

Tsiku ndi tsiku alendo ochokera kumaiko akunja komanso ena a m’dziko mwathu mom’muno amadzera msewuwu kuchoka pa Rumphi boma kupita ku Nyika National Park kukacheza ndi kukaona zinyama. Kunena zoona, Nyika ndi malo okongola kwambiri ndipo amene adapitako amafananiza malowa ndi ku Mangalande. Koma ndikukaika ngati akabwerera kwawo amakhalanso ndi chilakolako choti adzabwererenso tsiku lina kumalowa chifukwa msewu wake ndi wosautsa kwambiri.

Msewu wopita kumalo okopa  alendowa ndi umenewu
Msewu wopita kumalo okopa
alendowa ndi umenewu

Nthawi yachilimwe ngati ino si mabamphu ndi fumbi lake kuchokera paboma kukafika ku Nyika moti alendo amakfika ali mbuu kutuwa ngati nyau komanso atatopa kotheratu. Nthawi yadzinja ndiyenso kumakhala ntchito chifukwa si matope ake moti ena amangobwerera paboma osakafika ku Nyikako.

Komanso msewu wa Nyikawu ndiye wachidule kwa anzathu omwe amakhala ku Nthalire ndi Wenya m’boma la Chitipa. Utakhala kuti waikidwa phula ndiye kuti nawonso awomboledwa kumbali ya maendedwe. Sakazunguliranso ku Karonga mpaka kukafika paboma la Chitipa kenaka n’kumalumikiza kukafika kwawo.

Ife alimi timavutika kwambiri kupita ndi katundu wathu kumisika chifukwa cha kuonongeka kwa msewuwu komanso timalipira ndalama zambiri tikakwera galimoto.

Chonde, nafe ndife Amalawi, tithandizeni.

G.V.H. Mpasula,

Rumphi

Related Articles

Back to top button