Nkhani

Msika wa fodya utsekulidwa April

 

Misika yaikulu ya fodya m’dziko muno ikhoza kutsekulidwa sabata yachiwiri ya mwezi wa mawa, atero akuluakulu a bungwe lowona za fodya m’dziko muno la Tobacco Control Commission (TCC).

Fodya ndi mbewu yaikulu imene dziko lino limagulitsa kunja ndi kubweretsa ndalama zimene zimathandiza pa ntchito zina za boma.

Msika wa fodya wa okushoni
Msika wa fodya wa okushoni

Polankhula pa lamya kuchokera ku Lilongwe Lachiwiri, mkulu wa TCC Albert Changaya adati masikuwa ndiwongoganizira chabe popeza zokambirana zili mkati.

Apa Changaya adachenjeza alimi kuti misikayi ikatsekulidwa asamalitse ndi onyamula fodya ena omwe akumachita utambwali pobera alimi.

Iye adati onyamula fodya achinyengowa adabera alimi pafupifupi K1.4 biliyoni chaka chatha.

“Ena mwa onyamula fodya amanama malo omwe atengako fodyayu ngati uli mtunda waufupi potchula dera lakutali ndi cholinga chofuna kuba. Kafukufuku yemwe adapanga akatswiri athu odziwa kulondoloza zachuma adapeza kuti m’chaka chatha choka K1.4 biliyoni idapita,” Changaya adatero.

Apa adanenetsa kuti anthuwa adziwe kuti kwawo kwatha chifukwa bungweli lili pa kalikiliki wokhazikitsa ndondomeko zatsopano zothana ndi mchitidwewu.

“Tizigwiritsa ntchito nambala za zitupa za alimi zomwe pa Chingerezi timati zoning. Apa tizidziwa dera lomwe fodyayu akuchokera ndipo wonama aliyense azidziwika,” Changaya adatero. Iye adati  bungweli likukumana ndi onyamula fodyawa sabata yamawa kuti akambirane za ndondomeko zomwe zakhazikitsidwa pokonzanso zinthu.

Changaya adati TCC  laletsanso bungwe limodzi kukhala loyang’anira alimi lomwelonso lonyamula fodya.

Sabata zapitazi woyang’anira kampani ya Auction Group m’chigawo cha kumpoto, Joseph Kawinga adauza gulu la alimi akuluakulu a fodya ochokera m’chigawocho kuti ena mwa onyamula fodya amatenga fodya kuchokera kwa alimi ndi kungomusiya mmalo osungira katundu mumzinda wa Mzuzu mmalo mokasiya kumsika wa fodya.

Kawinga adati chifukwa cha kukhalitsa kwa fodyayu m’nyumbazi anthuwa amaluza ziphaso zoperekera fodya ndipo amakonzanso ziphaso zawo za bodza.

“Mwamwayi ziphaso zabodzazi zomwe nambala zake sizigwirizana ndi nambala za pa zitupa zenizeni za kumsika wathu wa fodya, timazidziwa ndipo sitilola kuti fodyayu agulitsidwe popereka chiletso mpaka zonse zitalongosoka,” adatero Kawinga.

Iye adapempha alimi kuti chaka chino ayesetse kupeza owanyamulira fodya okhulupirika oti akafikitsa mabelo awo kumsika wa fodya.

Mmodzi wa alimi akuluakulu a fodya mchigawochi Harry Mkandawire adati bungwe la TCC lichirimike pokonzanso ndondomekozi.

Fodya ndi mbewu yomwe dziko la Malawi limadalira pa chuma chake ndipo chaka chatha chokha dziko lino lidapeza $337.40 miliyoni (pafupifupi K253 biliyoni) litagulitsa fodyayu. n

Related Articles

Back to top button